YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 48

48
Awadandaulira Aisraele, awachenjeza, nalonjezana nao
1 # Yer. 5.2 Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m'zoona, pena m'chilungamo. 2#Aro. 2.17-23Pakuti adziyesa okha a mudzi wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israele; dzina lake ndi Yehova wa makamu. 3Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazichita izo, ndipo zinaoneka. 4#Eks. 32.9Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa; 5chifukwa chake ndinakudziwitsa ichi kuyambira kale; chisanaoneke ndinakusonyeza icho, kuti iwe unganene, Fano langa lachita izo, ndi chifaniziro changa chosema, ndi chifaniziro changa choyenga zinazilamulira. 6Iwe wachimva; taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzachinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kuchokera nthawi yino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe. 7Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa. 8Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire. 9#Mas. 78.38Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse. 10#Mas. 66.10; 1Pet. 1.7Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso. 11#Yes. 42.8; 43.25; Ezk. 20.9Chifukwa cha Ine ndekha, chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.
12 # Yes. 41.4 Mverani Ine, Yakobo ndi Israele, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womaliza. 13#Mas. 102.25Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m'mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi. 14#Yes. 44.28Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni. 15#Yes. 45.1-3Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yake. 16#Yes. 61.1Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m'tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake. 17#Mas. 32.8Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo. 18#Mas. 81.13; 119.165Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja; 19#Gen. 22.17; Hos. 1.10mbeu yakonso ikadakhala monga mchenga, ndi obadwa a m'chuuno mwako momwemo; dzina lake silikadachotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.
20 # Yes. 44.22-23; 52.11 Tulukani inu m'Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo. 21#Deut. 8.15Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika. 22#Yes. 57.21Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.

Currently Selected:

YESAYA 48: BLPB2014

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in