1
Mt. 7:7
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Compare
Explore Mt. 7:7
2
Mt. 7:8
Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Explore Mt. 7:8
3
Mt. 7:24
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.
Explore Mt. 7:24
4
Mt. 7:12
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Explore Mt. 7:12
5
Mt. 7:14
Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Explore Mt. 7:14
6
Mt. 7:13
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri.
Explore Mt. 7:13
7
Mt. 7:11
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
Explore Mt. 7:11
8
Mt. 7:1-2
“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.
Explore Mt. 7:1-2
9
Mt. 7:26
Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga.
Explore Mt. 7:26
10
Mt. 7:3-4
Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene m'maso mwako momwe muli chimtengo?
Explore Mt. 7:3-4
11
Mt. 7:15-16
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu?
Explore Mt. 7:15-16
12
Mt. 7:17
Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa.
Explore Mt. 7:17
13
Mt. 7:18
Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai.
Explore Mt. 7:18
14
Mt. 7:19
Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto.
Explore Mt. 7:19