1
Mlaliki 4:9-10
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu: Ngati winayo agwa, mnzakeyo adzamudzutsa. Koma tsoka kwa munthu amene agwa ndipo alibe wina woti amudzutse!
Compare
Explore Mlaliki 4:9-10
2
Mlaliki 4:12
Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa, koma anthu awiri akhoza kudziteteza. Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.
Explore Mlaliki 4:12
3
Mlaliki 4:11
Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana. Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?
Explore Mlaliki 4:11
4
Mlaliki 4:6
Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere, kuposa kukhala ndi manja awiri odzaza uli pa mavuto, ndipo uku nʼkungodzivuta chabe.
Explore Mlaliki 4:6
5
Mlaliki 4:4
Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
Explore Mlaliki 4:4
6
Mlaliki 4:13
Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo.
Explore Mlaliki 4:13