1
Mlaliki 5:2
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Usamafulumire kuyankhula, usafulumire mu mtima mwako kunena chilichonse pamaso pa Mulungu. Mulungu ali kumwamba ndipo iwe uli pa dziko lapansi, choncho mawu ako akhale ochepa.
Compare
Explore Mlaliki 5:2
2
Mlaliki 5:19
Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.
Explore Mlaliki 5:19
3
Mlaliki 5:10
Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo; aliyense amene amakonda chuma sakhutitsidwa ndi zimene amapeza. Izinso ndi zopandapake.
Explore Mlaliki 5:10
4
Mlaliki 5:1
Uzisamala mayendedwe ako pamene ukupita ku nyumba ya Mulungu. Upite pafupi kuti ukamvetsere mʼmalo mopereka nsembe ya zitsiru zimene sizizindikira kuti zikuchita zolakwa.
Explore Mlaliki 5:1
5
Mlaliki 5:4
Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako.
Explore Mlaliki 5:4
6
Mlaliki 5:5
Kuli bwino kusalumbira kusiyana ndi kulumbira koma osakwaniritsa lumbirolo.
Explore Mlaliki 5:5
7
Mlaliki 5:12
Wantchito amagona tulo tabwino ngakhale adye pangʼono kapena kudya kwambiri, koma munthu wolemera, chuma sichimulola kuti agone.
Explore Mlaliki 5:12
8
Mlaliki 5:15
Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake, ndipo monga iye anabadwira, adzapitanso choncho. Pa zonse zimene iye anakhetsera thukuta palibe nʼchimodzi chomwe chimene adzatenge mʼmanja mwake.
Explore Mlaliki 5:15