1
MATEYU 19:26
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
Linganisha
Chunguza MATEYU 19:26
2
MATEYU 19:6
Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.
Chunguza MATEYU 19:6
3
MATEYU 19:4-5
Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?
Chunguza MATEYU 19:4-5
4
MATEYU 19:14
Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.
Chunguza MATEYU 19:14
5
MATEYU 19:30
Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.
Chunguza MATEYU 19:30
6
MATEYU 19:29
Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.
Chunguza MATEYU 19:29
7
MATEYU 19:21
Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.
Chunguza MATEYU 19:21
8
MATEYU 19:17
Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.
Chunguza MATEYU 19:17
9
MATEYU 19:24
Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.
Chunguza MATEYU 19:24
10
MATEYU 19:9
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Chunguza MATEYU 19:9
11
MATEYU 19:23
Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba.
Chunguza MATEYU 19:23
Nyumbani
Biblia
Mipango
Video