Luka 23
23
Yesu wapelekedwa kwa Pilato
Matayo 27:1-2,11-14; Maluko 15:1-5; Yohana 18:28-38
1Ndiipo bwalo lonjhe lidaima ni kumpeleka Yesu kwa Pilato. 2Adayamba kumnamizila milandu pokamba, “Mundhu uyu tamuona niwanyenga wandhu ajhiko lathu, wakaniza wandhu kuti asamapeleka malipilo kwa mfumu wa ku Loma ni kujhichita iye kuti Kilisito Mfumu” 3Ndiipo Pilato wadamfunjha Yesu, “Eti iwe ni Mfumu wa Ayahudi?” Yesu wadamuyangha Pilato, “Iwe umwene nde wakamba.” 4Pilato wadakambila wakuluakulu ajhukulu ni gulu lonjhe lidali pamenepo, “Palibe cholakwa icho nichiona kwa mundhu uyu.” 5Nambho anyiiwo adachimikiza kukamba, “Mayaluzo yake yachita wandhu apanduke mu Yudea yonjhe. Wadayambila ku Galilaya ni chipano wali pano pa Yelusalemu.”
Yesu wapelekedwa kwa Helode
6Pilato yapo wadavela chimwecho, wadafunjha funjho, “Bwanji, mundhu uyu ni waku Galilaya?” 7Yapo wadajhiwa kuti Yesu wadali wajhiko ilo wamalamulila Helode, wadampeleka kwa Helode, nayo uyo wadali ku Yelusalemu ndhawi imeneyo.
8Helode wadakondwa kupunda yapo wadamuona Yesu. Kuyambila kale wadakhumbila kupunda kumuona Yesu ndande wadavela nghani zake. Iye Helode wamalindilila kumuona Yesu uku niwachita vodabwicha. 9Helode wadamfunjha Yesu mafunjho yambili, yayo Yesu siwadayanghepo ata limojhi. 10Ajhukulu wakuluakulu ni oyaluza thauko anyiawo adali adamnamizila mawu ya mbili Yesu. 11Ndiipo Helode ni asikali wake adamkwiicha Yesu kwa kumtukwana. Adamveka chovala cha chifumu, ni kumbweza kwa Pilato. 12Siku limenelo Helode ni Pilato adakhala mabwenji nambho kuyambila poyamba adali adani.
Yesu wahukumidwa kuphedwa
Matayo 27:15-26; Maluko 15:6-15; Yohana 18:39; 19:16
13Ndiipo Pilato wadasonghanicha wakuluakulu wa ajhukulu ni wandhu yawo adali pajha, 14wadakamba, “Mwampeleka mundhu uyu pano kumpacha mlandu, kuti wakwinjizila wandhu apanduke. Chipano vechelani, namfunjha pamaso panu ni naona kuti palibe cholakwa chilichonjhe cha kumuika mundhu uyu mmilandu. 15Osati inepe, ata Helode siwadaone kulakwa kulikonjhe, chimwecho walamula wambweze kwathu. Zenedi mundhu uyu siwadachite chindhu chilichonjhe chomchita walamulidwe kuphedwa. 16Chimwecho, sinimlange kumbula mikwapulo, alafu sinimsiilile.” 17Pakuti chidali chikhalidwe pasiku la pwando la Pasaka Pilato kwamasulila wandhu wandende mmojhi.
18Nambho wandhu wonjhe adayamba kukweza mvekelo kamojhi ni kukamba, “Waphedwe mundhu mmeneyo, tifuna umsiilile Balaba.” 19Balaba mmeneyo wadaikidwa mndende ndande kuchiticha wandhu kupanduka, mumujhi ni ndande ya kupha.
20Pilato wamafuna kumlekelela Yesu, chimwecho wadakamba nawonjho, 21nambho anyiiwo adayendekela kubula pokoso pokamba, “Wapachikidwe! Wapachikidwe!” 22Pilato wadakambilanjho kakatatu, “Bwanji walakwa chiyani mundhu uyu? Ndande, siniona cholakwa chilichonjhe icho chimchita kuti wapedwe. Chimwecho, sinilamule wabulidwe mikwapulo, alafu sinimsiilile.”
23Nambho wandhu adayendekela kukweza mvekelo waukulu kuti Yesu ifunika wapachikidwe pamtanda. Chimwecho, pothela mapokoso yao yadavomelezeka. 24Chimwecho, Pilato wadalamula kuti vofuna vawo vikwanilichidwe. 25Wadammasulila yujha mundhu wa mndende, uyo wadamangidwa ndande ya kupeleka kupanduka ni kupha wandhu. Uyo anyiiwo amafuna wamasulidwe, wadamchocha Yesu kwa anyiiwo kuti amchitile icho amachifuna.
Yesu wapachikidwa pamtanda
Matayo 27:32-44; Maluko 15:21-32; Yohana 19:17-27
26Wajha anghondo Yapo amapita nayo Yesu, adakomana ni mundhu mmojhi uyo wamatanidwa Simoni waku Kilene wamachoka kubwalo kwa mujhi. Adamgwila ni kumnyamulicha mtanda mmbuyo mwa Yesu. 27Chiwelengo chochuluka cha wandhu chimamchata Yesu, adalimo ni wachikazi yawo amamlilila ni kumdandaulila. 28Yesu wadang'anamukila ni kwakambila, “Anyiimwe Anyamaye aku Yeslusalemu, msadanililila ine, nambho mjililile mwachinawene wake ni wana wanu. 29Pakuti nyengo itokujha iyo simukambe, ‘Ali ni mwawi wachikazi ambende, yawo siadabalepo ni mawele yake siyadayamwichepo!’ 30Ndhawi imeneyo, wandhu sayakambile mapili, ‘Tigweleni,’ ni timapili, ‘Tivinikileni.’ 31Pakuti ngati anichitila chimwechi ine sinidalakwe chalichonjhe, siamchitile chiyani mundhu walakwa?”
32Kudali ni wandhu wina awili owananga adapita nao akaphedwe pamojhi ni Yesu. 33Yapo adafika pamalo yapo patanidwa Fuvu la Mutu, kumalo kumeneko adampachika Yesu pamojhi ni wandhu wajha owananga. Mmojhi kwene ni mnjake kumanjele. 34Yesu wadakamba, “Atate, mwalekelele wandhuwa, pakuti sajhiwa icho achichita.” Ndiipo adagawana njhalu zake kwa kuchita gudugudu. 35Wandhu adangoimilila pampajha naampenya. Ni achogoleli Ayahudi adamkwiicha Yesu pokamba, “Wadaombola wina! Chipano wajiombole mwene wake, ngatidi ni iye ni Kilisito, wosanghidwa ni Mnungu!” 36Asikali nawo adaja, adamkwiicha, adampelekela divai yowawa, 37Niayiiwo adamkambila, “Ngati zenedi iwe ni Fumu wa Ayahudi jhiombole umwene.”
38Chibao chidali pamwamba pa mtanda wake chidalembedwa chimwechi, UYU NDE FUMU WA AYAHUDI.
39Mmojhi wa wajha owananga adapachikidwa mmitanda pamojhi ni Yesu wadamtukwana, niwakamba, “Bwanji, iwe sinde Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu? Jhiombole mwene utiombole ni ife.” 40Nambho owananga mnjake wadamnyindila, wadakamba, “Bwanji, iwe suopa Mnungu ata pang'ono? Pakuti iwe nawe wapachikidwa ngati iye. 41Iwe ni ine tafunika yaya, ndande yaya nde mkokolo wa volakwa vathu. Nambho mundhu uyu siwadachite cholakwa chilichonjhe.” 42Ndiipo yujha owananga wadamkambila Yesu, “Imwe Ayesu! Mnikumbukile yapo simulowe mu Ufumu wanu.” 43Yesu wadamuyangha, “Nikukambila uzene, lelolino siukale pamojhi ni ine kumwamba.”
Yesu wamwalila
Matayo 27:45-56; Maluko 15:33-41; Yohana 19:28-30
44Idali ngati saa sita usana, mdima udalivinikila jhiko lonjhe mbaka saa tisa, 45pakuti jhuwa lidasiya kuwala, paziya la nyumba ya Mnungu lidang'ambika pakatikati kuyambila kumwanba mbaka panjhi. 46Yesu wadakweza mvekelo, wadakamba, “Atate, mzimu wanga ni uika mmanja mwanu.” Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, wadamwalila.
47Yujha Wamkulu wa asikali yapo wadaona yayo yachokela, wadamtamanda Mnungu pokamba, “Zenedi mundhu uyu wadali wavomelezeka pachogolo pa Mnungu.” 48Gulu la wandhu yawo adakomana pajha dala apenye ivo vidachitika, adabwela kumakomo, uku ni adajhibulabula vidale vawo kwa chisoni. 49Anyiwajha wonjhe yawo amamjhiwa pamojhi ni wachikazi wajha amamchata kuchokela ku Galilaya, adaima patali kupenya vindhu ivo vimachitika.
Kuzikidwa kwa Yesu
Matayo 27:57-61; Maluko 15:42-47; Yohana 19:38-42
50Padali mundhu mmojhi uyo wamatanidwa Yusufu, iye wadali mmojhi wa wandhu a Bwalo lalikulu la Ayahudi, mundhu mmeneyo wadali wovomelezeka pachogolo pa Mnungu. 51Iye siwamavomeleze ni malamulo ya bwalo ni vichito vao. Mundhu uyu wamachokela ku mujhi wa Alimataya ni wamaulindilila Ufumu wa Mnungu. 52Ndiipo Yusufu wadapita kwa Pilato kumpembha kuti wapachidwe chitanda cha Yesu. 53Iye wadalichicha chitanda cha Yesu kuchokela pajha pamtanda. Wadalivilingila sanda yoyela ya mtengo waukulu, ni kuliika chitanda mu manda ilo lidasepedwa pamwala waukulu, umo simdaikidwemo chitanda chilichonjhe. 54Siku limenelo lidali siku lojhikonjekela, ndande idali kuyamba kwa siku lopumulila.
55Wachikazi wajha adamchata Yesu kuchokela ku Galilaya, adamchata Yusufu, ni adapaona pamalo yapo chidazikidwa chitanda cha Yesu. 56Ndiipo adapita kukhomo. Adakonjekela mafuta yo nunghila ni mafuta ya kuchinyeka chitanda cha yesu. Siku lopumulila adapumulila ngati umo idalamulidwa ni thauko.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Luka 23: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: