Luka 21
21
Njhembe ya maye uyo wafedwa ni mmunake
Maluko 12:41-44
1Yesu yapo wadapenyechecha, wadaona wandhu wopata naathila njhembe zawo mu bokosi lo sungila ndalama za nyumba ya Mnungu, 2wadamuonanjho maye mmojhi wosauka uyo wafedwa ni mmunake niwathila senti ziwili mbokosi mujha. 3Yesu wadakamba, “Zenedi nikukambilani, maye wosaukayu uyo wafedwa ni mmunake, wathila njhembe yochuluka kupitilila wandhu wonjhewa. 4Pakuti wandhu wina amchochela njhembe Mnungu kuchokana ni kuchuluka kwa chuma chao, nambho maye wofedwa wammuna wachocha kuchokana ni kusauka kwake vonjhe va kumthangatila pa umoyo wake.”
Yesu walosa kughomoledwa kwa nyumba ya Mnungu
Matayo 24:1-2; Maluko 13:1-2
5Woyaluzidwa wina a Yesu amakamba kuusu ni miyala yabwino iyo idakwadilicha Nyumba ya Mnungu ni njhembe izo wandhu amamchochela Mnungu. Nambho Yesu wadaakambila, 6“Yonjhe yaya muyaona yapa, masiku siyafike, palibe mwala uwo siukhalile pamwamba pa unjake, ndande yonjhe siyagomeledwe ni kutaidwa panjhi.”
Vizindikilo va siku zo thela
Matayo 24:3-14; Maluko 13:3-13
7Oyaluzidwa wake adamfunjha, “Oyaluza mtikambile, sivichokele chakanji vindhu vimenevi, ni vizindikilo vanji sivilangize kuti vindhu vimenevo sivichitike?”
8Yesu wadayangha, “Chenjelani, kuti musadanyengedwa. Pakuti wandhu ambili siajhe naajhichita kuti anyiiwo nde ine, naakamba, ‘Ine nde Kilisito,’ kapina, ‘Nyengo ya yameneyo ili pafupi.’ Nambho anyiimwe simdaachata. 9Nambho yapo simuvele nghani za nghondo ni kupanduka kwa wandhu, musadaopa ndande yameneyo yafunika yachokele poyamba, nambho mathelo siyachokela nyengo imeneyo.”
10Ndiipo Yesu wadayendekela wadakambila, “Wandhu ajhiko limojhi sabulane ni wandhu ajhiko linjake, ni ufumu umojhi siubulane ni ufumu unjake. 11Sikukhale ni chimtingiza cha chikulu cha ndhaka, ni njala yaikulu ni matenda yoofya kila kumalo. Sikuchokele vindhu voofya ni vizindikilo vavikulu kuchokela kumwamba. 12Nambho yakali osachokele yameyo, sakugwileni ni kukuvutichani ni sakupelekeni mmnyumba za mapembhelo ni kukuikani mundende. Simupelekedwe pachogolo pa mafumu ni amaulamulilo ndande ya kunichata ine, 13nambho kwa anyiimwe imeneyo nde siikhale nyengo yo lalikila Uthenga wabwino kwa anyiiwo. 14Nambho msakhala ni mandha kuti simukambe chiyani kuti mujhipulumuche, 15Pakuti ine sinikupacheni mawu pamojhi ni njelu, palibe uyu siwakhoze kulimbana ni anyiimwe kapina kukuchuchani. 16Obala wanu, achabale, achanjanu ni abwenji wanu sakung'anamukeni, ni wina pakati panu saphedwe. 17Simuipilidwe ni wandhu wonjhe ndande ya kunichata ine. 18Nambho, simpata chiwonongeko chalichonjhe icho sichikhale muyaya. 19Nambho uyo siwalimbe mtima mbaka pothela siwakhale ni umoyo wa muyaya.”
Yesu walosa kuusu kughomoledwa kwa Yelusalemu
Matayo 24:15-21; Maluko 13:14-19
20“Yapo simuone kuti mujhi wa Yelusalemu wazungululidwa ni asikali, jhiwani kuti masiku ya kughomoledwa kwake yawandikila. 21Ndhawi imeneyo yawo ali ku Yudea athawile kuphili, ni yawo ali mmujhi wa Yelusalemu achoke kubwalo, ni yawo ali kumunda sadalowa mmujhi umenewo. 22Ndande, masiku yameneyo siyakhale, ‘Masiku ya Chilango,’ dala kukwanilicha yonjhe yalembedwa Mmalembo Yoyela. 23Savutike kupunda yawo ali ni pathupi ni yawo ayamwicha pamasiku yameneyo! Ndande sikukhale mavuto yayakulu mjhiko ni mbhwayi ya Mnungu siikhale kwa wandhu amjhiko ili la Yudea. 24Wandhu wina siaphedwe kwa upanga, wina satengedwe ngati omangidwa ni kupelekedwa mmaiko yina. Ni mujhi wa Yelusalemu siulamulidwe ni wandhu osati Ayahudi, mbaka masiku yao yolamula yapo siyakwane.”
Kubwela kwa Mwana wa Mundhu
Matayo 24:29-31; Maluko 13:24-27
25“Sikukhale ni vizindikilo kujhuwa, kumwezi ni ndhondwa. Wandhu ajhiko lapanjhi saalage kupunda ni saakhale ni mandha yapo savele mtungulu ni kuyamila kwa mafunde ya nyanja yamchele. 26Wandhu saakomoke kwa mandha yayakulu, poona vindhu ivo sivionekane pajhiko. Pakuti vindhu vonjhe va mbhavu za kumwamba sivitingizike. 27Ndhawi imeneyo sianione ine Mwana wa Mundhu ninijha mmitambo, najhala mbhavu ni ulemelelo wochuluka. 28Vindhu ivi yapo siviyambe kuchokela, mdaime nganganga nimkweza mitu yanu kumwamba, pakuti uomboli wanu wawandikila.”
Mayaluzo kuchokana ni mtengo wa mkuyu.
Matayo 24:32-35; Maluko 13:28-31
29Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake mfano uwu, “Ganizilani mtengo wa mkuyu ni mitengo ina yonjhe. 30Yapo uyamba kuphukila machamba, mwachinawenewake mjhiwa kuti nyengo ya mwavu yakwana. 31Chinchijha, yapo simuone vindhu vimenevo nivichokela, mujhiwe kuti Ufumu wa Mnungu wawandikila.”
32“Kukambilani, ambadwa uwo siuvione vindhu ivi siutha mbaka yapo vindhu ivi yapo sivichokele. 33Kumwamba ni jhiko lapanjhi sivipite, nambho mawu yanga siyapita ata pang'ono.”
Ifunika kuchezelela
34“Mchenjele, mitima yanu siidalemeledwa ni ludyo ni kulojhela ni kulaga ndande ya umoyo uno, dala siku lijha silidakuphezani anyiimwe mwachizulumukila. 35Pakuti siku limenelo silaafikile wandhu wonjhe yao akhala pajhiko lonjhe lapanjhi. 36Mchezelele ni kupemphela nyengo zonjhe kuti mpheze mbhavu za kupulumuka yonjhe yayo siyachokele, kuti mukhoze kuima pamaso pa Mwana wa Mundhu.”
37Yesu wadali kuyaluza wandhu mnyumba ya Mnungu ndhawi zonjhe za usana, kila ujhulo wamapita kuphili la Mizeituni ni kukhala kumeneko usiku njenjenje. 38Wandhu wonjhe amalawila umawamawa ni kupita ku Nyumba ya Mnungu kumvechela Yesu.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Luka 21: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: