Vichito 7
7
Sitefano watojhiteteza
1Basi mjhukulu wamkulu wadamfunjha Sitifano, “Bwanji, vindhu ivi ni vazene?”
2Sitifano wadayangha, “Achaabale wanga ni achatate wanga, mnivechele! Mbuye wathu Ibulahimu yapo wadali wakali osapite kukhala ku Halani, Mnungu wa ulemelelo wadamuonekela iye ku Mesapotamiya. 3Mnungu wadamkambila, ‘Asiye wandhu wako ni jhiko ni upite ku jhiko ilo sinikulangize.’ 4Chimwecho Ibulahimu wadachoka mujhiko la Kalidayo ni kupita kukhala ku Halani. Atate wake Ibulahimu adamwalila, Mnungu wadamchocha kumeneko ni kujhanayo mu jhiko lino ilo anyiimwe mukhala ndhawi zino. 5Mnungu siwadampache chilichonjhe mu jhiko lino, siwadampache ata pamalo poikapo mapazi yake. Nambho Mnungu wadaahidi kuti iye ni mbadwa wake pambuyo pake siakhale mjhiko muno, ata ngati nyengo imeneyo Ibulahimu wadalibe mwana. 6Mnungu wadamkambila chimwechi, ‘Mibadwa yako siikhale ku jhiko la chilendo, siachitidwe kukhala akapolo ni kuchitidwa voipa kwa vyaka miya zinayi. 7Nambho ine siniliwanange jhiko lijha silaavutiche ngati akapolo. Pambuyo pake siachoke mjhiko limenelo ni kunilambila pamalo yapa.’ 8Ndiipo Mnungu wadachita chipangano ni Ibulahimu cha mdulidwe chikhale chizindikilo cha chipangano chimenecho. Nayo Ibulahimu wadambala Isaka ni kumchitila mdulidwe siku la nane pambuyo po badwa. Niiye Isaka wadamchita mdulidwe Yakobo mwana wake, ni Yakobo wadachita chimwecho kwa azee wathu khumi ni awili.”
9“Wana a Yakobo adamuonela njhanje mbale wao Yusufu, chimwecho adamgulicha kuti wakhale kapolo ku jhiko la Misili. Nambho Mungu wadali pamojhi ni iye. 10Amnungu adamuombola kuchokela ku mavuto yake yonjhe yayo yadampata, ni wadampacha mwawi ni njelu yapo wadaima pamaso pa Falao, mfumu wa Misili, uyo wadamuika kuti wakhale mlamuli wa jhiko la Misili, ni mlamuli wa nyumba yonjhe ya chifumu. 11Ndiipo kudali njala mu jhiko lonjhe la Misili ni Kaanani, iyo idapeleka kuvutika kwa kukulu. Ni achaatate wathu saadakhoze kupata chakudya. 12Basi Yakobo wadavela kuti kuli chakudya ku Misili, wadaatuma wana wake yawo ali achambuyathu kukayendela uti. 13Yapo adapita kakawili, Yusufu wadajhijhiwicha kwa achaabale wake, ni mfumu wa ku Misili wadaajhiwa achaabale a Yusufu. 14Chimwecho, Yusufu wadapeleka uthenga kwa Yakobo atate wake, kwaakambila iwo ni wandhu wonjhe a kwake kuti ajhe ku Misili. Wonjhe pamojhi adali wandhu sabini ni asano. 15Ndiipo Yakobo wadapita ku Misili, uko iye ni achanawake adafela. 16Matupi yao yadabwezedwa ku Shekemu, uko adazikidwa mviliza ivo wadavigula Ibulahimu kuchokela kwa wana wa Hamoli kwa ndalama.”
17“Yapo idakwana ndhawi yokwanilicha yajha Mnungu wadaamuahidiya Ibulahimu, chiwelengo cha wandhu mujha mu Misili chidachuluka ni kukula. 18Ndiipo wadachokela mfumu mwina uyo wadayamba kulamulila jhiko la Misili, uyo siwamamjhiwe Yusufu. 19Mfumu mmeneyo wadaachita kuipa azee wathu ni pa kuwakakamiza kwaataya wana wao akhanda kuti afe. 20Ndhawi imeneyo nde ndhawi iyo wadabadwila Musa, nayo wadali mwana uyo wadamuona kuti ni wabwino. Iye wadaleledwa kwa ndhawi ya miezi itatu. 21Yapo adalepela kumbisa munyumba kwa ndhawi yaitali, adamuika kubwalo, ni mwali wa Falao wadamtenga ni kumulela ngati mwana wake mwenewake. 22Musa wadayaluzidwa ekima zonjhe za ku Misili, wamakhoza kukamba bwino ni kuchita vindhu zosiyana siyana.”
23“Musa yapo wadakwana vyaka alobaini wadalamula kwaayendela achaabale wake a Izilaeli kupita kuona vindhu vanji ivo amachitidwa. 24Kumeneko wadamuona mmojhi wa aizilaeli niwavutichidwa ni a Misili, chimwecho wadapita kumthandiza yujha Mwizilaeli, wadambula yujha m Misili ni kumupha kubwezela mbwezo. 25Musa wamaganiza kuti achaabale wake adakajhiwa kuti Mnungu wamtumila kwaaombola, nambho anyiiwo sadajhiwe chimwecho. 26Siku lidachatila Musa wadaakomana a Izilaeli awili naabulana, wadayesa kwaavanichana pakwaakambila, ‘Anyiimwe ni achabale, bwanji mufuna kupwetekana mwachinawene?’ 27Nambho mwina yujha wamambula mnjake wadamkangha Musa kutali, wadamfunjha, ‘Yani uyo wakuika iwe kukhala mchogoleli ni mlamuli wathu? 28Bwanji, ufuna kunipha ngati umo udamphela yujha Mmisili jhulo?’ 29Musa yapo wadavela chimwechi, wadathawa ni kupita kukhala mjhiko la Midiyani. Kumeneko Musa wadabala wana awili waachimuna.
30“Yapo vidapita vyaka alobaini, atumiki a kumwamba a Mnungu adamchokela Musa mnjila ya fukutu ilo limakwelela moto kuphululu kujha pafupi ni phili la Sinayi. 31Musa wadazizwa yapo wadaona vindhu vimenevo, wadasendelela pafupi ni fukutu lijha kuti waone bwino. Nambho wadavela mvekelo wa Ambuye niakamba, 32‘Ine ni Mnungu wa azee wako a kale, Mnungu wa Ibulahimu, Isaka ni Yakobo.’ Musa wadatendhemela kwa mandha ni wadayese kupenyanjho. 33Mnungu wadamkambila Musa, ‘Vula malapasi yako, pakuti pamalo pano waima ni pamalo Poyela. 34Nayaona mavuto ya wandhu wanga kujha ku Misili. Navela chililo chao, chipano najha kwaombola. Basi chipano, sinikutume ku jhiko la Misili.’”
35“Musa mmeneyo nde yujha wandhu a Ku Izilaeli adamkana yapo adakamba, ‘Yani uyo wakuika iwe kukhala mchogoleli ni mlamuli wathu?’ Kwanjila ya yujha Mtumiki wa Kumwamba wa Mnungu uyo wadamchokela Musa ku fukutu limakwelela moto, Mnungu wadamtuma Musa wakhale mchogoleli ni muomboli. 36Nde uyo wadaachogoza wandhu kuchoka ku Misili, niwachita vodabwicha ni vozizwicha mu Misili ni pa Nyanja ya Shamu, ni muphululu mu ndhawi ya vyaka alobaini. 37Musa nde uyo wadaakambila wandhu a ku Izilaeli, ‘Mnungu siwakusanghulileni mlosi ngati umo wanitumila ine, ni siwachokele pakati panu mwachinawene.’ 38Aizilaeli yapo adasonghana kujha ku phululu, Musa nde uyo wadalipo kumeneko ngati mthenga pakati pa azee wathu ni yujha mtumiki wa kumwamba wa Mnungu adakamba naye kuphili la Sinai, ndeuyo wadapachidwa mau yayo yapeleka umoyo.”
39“Nambho azee wathu adakana kumuvela Musa, adambwanyizila kutali ni kufuna kuti abwelelenjho ku Misili. 40Chimwecho adamkambila Aloni, ‘Tikonjele minungu iyo siitichogoze. Pakuti sitijhiwa icho chamchokela Musa uyo watichogoza kuchokela ku Misili!’ 41Pamenepo nde yapo adajhikonjela chiboliboli cha mwana wa ng'ombe, adachichochela njhembe ni kuchita phwando kuchikondwela chijha chiboliboli. 42Ndipo Mnungu wadaasiya ni kwaachita ajhilambila ndhondwa za kumwamba ngati umo yalembedwela muchikalakala cha alosi,
‘Anyiimwe wandhu a ku Izilaeli!
Osati ine mdanichochela njhembe yophyeleza
kwa vyaka alobaini mu phululu?
43Anyiimwe nde mudatenga hema la mnungu Moleki,
ni viboliboli va ndhondwa ya mnungu wanu Lefani,
viboliboli ivo mudavikonja, nde ivo mdavilambila.
Chimwecho, inenjho sinikupelekeni ku ukapolo kutali kupitilila jhiko la Babiloni.’”
44Achaatate wathu adali ni hema lijha limalangiza kuti Mnungu wali pamenepo. Lidakonjedwa ngati umo Mnungu wadamkambila Musa wachite, kuchokana ni umo wadalangizidwa kuti walikonje. 45Pambuyo pake, azee wathu wajha adalandilana hema limenelo ayiiwo kwa anyiiwo mbaka Yoshuwa yapo wamachogoza, adalanda jhiko kuchokela kwa maiko yajha yadatopoledwa ni Mnungu pamaso pao. Hemalo lidakhala mjhiko limenelo mbaka pa ndhawi iyo Daudi. 46Daudi wadakondeledwa ni Mnungu, ni wadapembha Mnungu kuti wamloleze wammangile nyumba umo iye ni Aizilaeli wonjhe akhoza kumlambila. 47Nambho Solomoni nde uyo wadamanga nyumba ya Mnungu. 48Ata chimwecho, Mnungu wamkulu wa Kumwamba siwakhala mnyumba yomangidwa ni manja ya mundhu, ngati umo mlosi wakambila,
49“Ambuye akamba, ‘Kumwamba ni mpando wanga wachifumu,
ni pajhiko lapanjhi ni malo ya kuikapo miyendo yanga.
Nyumba yamtundu wanji iyo simunimangile ine?
Kapina malo yanga yopumulilamo siyakhale yati?
50Bwanji, vindhu vonjhevi sinidavimange ine kwa manja yanga?’”
51Sitefano wadaendekela kukamba, “Anyiimwe ni wandhu a mbwinya, mitima ni makutu yanu yali ngati wandhu yawo samjhiwa Mnungu, ndhawi zonjhe simusiya kulimbana ni Mzimu Woyela, ngati umo adachitila azee wanu akale. 52Bwanji, pali mlosi yuti uyo achambuye wanu saadamvutiche? Adaapha yawo Mnungu wadatuma akauzile kujha kwake yujha wovomelezeka. Namwenjho muli wandhu yawo mumunga'anamuka ni kumpha. 53Anyiimwe nde anyiyawo mudalandila thauko, ilo lidapelekedwa ni atumiki akumwamba a Mnungu, nambho simchita ngati umo ifunikila.”
Sitefano wapedwa
54Anyiwajha Azee a bwalo yapo adavela chimwechi, adakwiya kupunda adamkukutila mano kwambwayi Sitefano. 55Nambho Sitifano, wali wojhala Mzimu Woyela, wadapenya kumwamba ni wadaona ulemelelo wa Mnungu, ni Yesu wadakhala ku malo ya ulemu ya Amnungu. 56Wadaakambila, “Vechelani! Niona kumwamba kwachekuka ni Mwana wa Mundhu wakhala kujhanja la kwene la Mnungu!”
57Nambho anyiiwo adapunda kubula phokoso lalikulu, adacheka makutu, ndiipo wonjhe adamlumbhila kwa pamojhi. 58Adamtaya kubwalo kwa mujhi ni kuyamba kumponya miyala. Wajha amboni adaika njhalu zao pa miyendo ya mnyamata mmojhi uyo wamatanidwa Saulo kuti wachite ulonda. 59Yapo amaendekela kumpmonya miyala, Sitifano wadapembhela, “Ambuye Yesu, landilani mzimu wanga!” 60Wadagwada ni kulila kwa mvekelo wa waukulu, “Ambuye, musadalamula wandhu yawa kwa machimo yaya.” Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, wadamwalila.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Vichito 7: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: