Chimwecho Ananiya wadapita, wadalowa mkati umo wadali Saulo ni wadamsanjika jhanja, niwakamba, “Mbale wanga Saulo, Ambuye Yesu yawo adakutulukila panjila, anituma kwako kuti uonenjho ni kujhazidwa Mzimu Woyela.” Pomwepo vidagwa vindhu ngati mamba kuchokela mmaso mwake, wadakhoza kuona, wadaima ni wadabatizidwa.