Mk. 6:41-43
Mk. 6:41-43 BLY-DC
Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthuwo. Anthu onse aja adadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala za buledi ndi za nsomba zija nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.


