Mk. 15

15
Yesu ku bwalo la Pilato
(Mt. 27.1-2, 11-14; Lk. 23.1-5; Yoh. 18.28-38)
1M'maŵa kutangocha, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi aphunzitsi a Malamulo, pamodzi ndi ena onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda adapanga upo. Adammanga Yesu napita naye kwa Pilato. 2Pilatoyo adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha.” 3Akulu a ansembe aja adayamba kumneneza zambiri. 4Pilato adamufunsanso kuti, “Kodi ulibe poyankha? Ona zonse zimene akukunenezazi.” 5Koma Yesu sadayankhenso kanthu, kotero kuti Pilato adadabwa.
Pilato agamula kuti Yesu aphedwe
(Mt. 27.15-26; Lk. 23.13-25; Yoh. 18.39—19.16)
6Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira mkaidi mmodzi, yemwe Ayudawo ankapempha. 7Panali munthu wina, dzina lake Barabasi, amene anali m'ndende pamodzi ndi anthu ena chifukwa choukira Boma ndi kupha anthu. 8Tsono chikhamu cha anthu chidabwera, nkuyamba kupempha Pilato kuti aŵachitire zomwe adaazoloŵera. 9Pilato adaŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?” 10Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo akulu a ansembewo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe. 11Koma akulu a ansembewo adasonkhezera anthu onse aja kuti apemphe kuŵamasulira Barabasi. 12Tsono Pilato adaŵafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndichite naye chiyani uyu amene mukuti ndi Mfumu ya Ayudayu?” 13Anthuwo adafuula kuti, “Mpachikeni pa mtanda!” 14Pilato adaŵafunsa kuti, “Adalakwanji?” Koma iwo adafuula koposa kuti, “Mpachikeni pa mtanda!” 15Choncho Pilato, pofuna kukondwetsa anthuwo, adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda.
Asilikali achita Yesu chipongwe
(Mt. 27.27-31; Yoh. 19.2-3)
16Pamenepo asilikali adaloŵetsa Yesu m'bwalo, kunyumba kwa bwanamkubwa, nasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao. 17Adamuveka chovala chofiirira, naluka nsangamutu yaminga nkuiika pamutu pake. 18Kenaka adayamba kumampatsa moni kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.” 19Ankamumenya m'mutu ndi ndodo, namamthira malovu, nkumamugwadira monyodola. 20Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija, namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.
Yesu apachikidwa pa mtanda
(Mt. 27.32-44; Lk. 23.26-43; Yoh. 19.17-27)
21 # Aro. 16.13 Pa njira adakumana ndi munthu wina, amene ankadutsa pamenepo kuchokera ku midzi. Munthuyo anali Simoni wa ku Kirene, bambo wake wa Aleksandro ndi Rufu. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu. 22Iwowo adapita naye Yesuyo ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti “Malo a Chibade cha Mutu.”) 23Adaafuna kumpatsa vinyo wosanganiza ndi mure#15.23: vinyo wosanganiza ndi mure: Anali mankhwala oletsa kupweteka. kuti amwe, koma Iye adakana.
24 # Mas. 22.18 Atampachika pa mtanda, adagaŵana zovala zake. Adaachita maere kuti aone zimene aliyense atenge. 25Pamene adampachika pa mtanda, nkuti nthaŵi ili 9 koloko m'maŵa. 26Mau osonyeza mlandu womuphera, adaaŵalemba motere, “Mfumu ya Ayuda.” 27#Yes. 53.12Pamodzi ndi Yesu adaapachikanso pa mitanda zigaŵenga ziŵiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere.
[ 28Motero zidachitikadi zimene mau a Mulungu adaanena kuti, “Adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo.”]
29 # Mas. 22.7; 109.25; Mk. 14.58; Yoh. 2.19 Anthu amene ankadutsa pamenepo ankamunyodola. Ankapukusa mitu nkumanena kuti, “Ha, suja iwe unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’ 30Tadzipulumutsatu, tsika pamtandapo!” 31Nawonso akulu a ansembe ankamuseka, nkumauzana ndi aphunzitsi a Malamulo kuti, “Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye yemwe! 32Uja ankati ndi Mpulumutsi wolonjezedwayu, Mfumu ya Aisraele, atatsikatu tsopano pamtandapa, kuti tiwone ndi kumkhulupirira!” Ndiponso amene adaŵapachika pamodzi naye aja ankamunyoza.
Kufa kwa Yesu
(Mt. 27.45-56; Lk. 23.44-49; Yoh. 19.28-30)
33Nthaŵi itakwana 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko. 34#Mas. 22.1 Tsono nthaŵi ili 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?” 35Atamva mauwo, ena amene adaaimirira pamenepo adati, “Tamverani, akuitana Eliya.” 36#Mas. 69.21Motero wina adathamanga nakaviika chinkhupule m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. Anzakewo adati, “Taima, tiwone ngati Eliyayo abweredi kudzamtsitsa.” 37Koma Yesu adafuula kwakukulu, natsirizika.
38 # Eks. 26.31-33 Chinsalu chochinga#15.38: Chinsalu chochinga: Onani pa Eks. 26.33. chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. 39Mkulu wa asilikali amene adaaimirira pomwepo kuyang'anana naye, ataona kuti Yesu watsirizika akufuula chotero, adati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.” 40#Lk. 8.2, 3Patali poteropo padaali azimai, akungoyang'anitsitsa. Ena mwa iwo anali Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe wamng'ono uja ndi wa Yosefe, ndiponso Salome. 41Azimaiŵa ankatsata Yesu pamene Iye anali ku Galileya, ndi kumamtumikira. Padaalinso azimai ena ambiri omwe adaabwera naye ku Yerusalemuko.
Yesu aikidwa m'manda
(Mt. 27.57-61; Lk. 23.50-56; Yoh. 19.38-42)
42Tsopano chisisira chinali chitagwa. Ndiye popeza kuti linali Lachisanu, tsiku lokonzekera Sabata,#15.42: tsiku lokonzekera Sabata: Ayuda amaŵerenga tsiku kuyambira pa kuloŵa kwa dzuŵa. 43Yosefe wa ku Arimatea adafika. Adaali mkulu wodziŵika ndithu, wa m'Bwalo Lalikulu la Ayuda. Nayenso ankayembekeza Ufumu wa Mulungu. Tsono iye adalimba mtima, napita kwa Pilato kukapempha kuti ampatsire mtembo wa Yesu. 44Pilato adaadabwa kumva kuti Yesu wafa kale. Choncho adaitanitsa mkulu wa asilikali uja, namufunsa kuti, “Kodi Yesu wafa kaledi?” 45Mkulu wa asilikaliyo atavomera, Pilato adamlola Yosefe kuti akatenge mtembowo. 46Yosefeyo adagula nsalu yoyera yabafuta, natsitsa mtembo uja nkuukuta ndi nsaluyo. Adauika m'manda ochita chosema m'thanthwe, kenaka adagubuduzira chimwala pa khomo kutseka pamandapo. 47Maria uja wa ku Magadala, ndi Maria mai wa Yosefe, ankaona kumene adamuika Yesu.

اکنون انتخاب شده:

Mk. 15: BLY-DC

های‌لایت

کپی

مقایسه

به اشتراک گذاشتن

None

می خواهید نکات برجسته خود را در همه دستگاه های خود ذخیره کنید؟ برای ورودثبت نام کنید یا اگر ثبت نام کرده اید وارد شوید