Mk. 12:43-44
Mk. 12:43-44 BLY-DC
Tsono Yesu adaitana ophunzira ake naŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa anthu ena onseŵa, amene akuponya ndalama m'bokosimu. Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”


