Mk. 12:41-42
Mk. 12:41-42 BLY-DC
Tsiku lina Yesu adaakhala pansi kuyang'anana ndi bokosi loponyamo ndalama zopereka ku Nyumba ya Mulungu. Ankayang'anitsitsa m'mene anthu ankaponyera ndalama zao. Anthu ambiri achuma ankaponyamo ndalama zambiri. Koma padafika mai wina wamasiye, wosauka. Iyeyu adangoponyamo tindalama tiŵiri.


