Mk. 12:29-31
Mk. 12:29-31 BLY-DC
Yesu adamuyankha kuti, “Lamulo lalikulu ndi ili, ‘Tamverani, inu Aisraele, Chauta, Mulungu wathu, Iye yekha ndiye Mulungu. Motero, uzikonda Chauta, Mulungu wakoyo, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse.’ Lamulo lachiŵiri lake ndi ili, ‘Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.’ Palibe lamulo lina loposa malamulo ameneŵa.”


