Mt. 6
6
Za kupereka zachifundo
1 #
Mt. 23.5
“Chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba.
2“Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. 3Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe zimene dzanja lako lamanja likuchita. 4Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziŵa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.
Za kupemphera
(Mk. 11.25-26; Lk. 11.2-4)
5 #
Lk. 18.10-14
“Pamene mukupemphera, musachite monga anthu achiphamaso aja. Iwowo amakonda kuimirira ndi kupemphera m'nyumba zamapemphero ndi pa mphambano za miseu yam'mizinda. Amachita zimenezi kuti anthu aŵaone. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. 6Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.
7 #
Mphu. 7.14
“Pamene mukupemphera, musamangobwerezabwereza mau monga amachitira anthu akunja. Iwowo amayesa kuti akachulukitsa mau choncho, ndiye pamene Mulungu aŵamvere. 8Inu musamatero ai, pakuti Atate anu amadziŵa zimene mukusoŵa, inu musanapemphe. 9Nchifukwa chake popemphera muziti,
“Atate athu akumwamba,
dzina lanu lilemekezedwe.
10Ufumu wanu udze.
Kufuna kwanu kuchitidwe,
monga kumwamba chomwechonso pansi pano.
11Mutipatse ife lero chakudya chathu chamasikuwonse.
12Mutikhululukire ife machimo athu,
monga ifenso takhululukira otilakwira.
13Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa,
koma mutipulumutse kwa Woipa uja.”#6.13 …koma mutipulumutse kwa Woipa uja: Kapena…koma mutipulumutse ku zoipa.
[Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero
ndi zanu kwamuyaya.
Amen.]
14 #
Mk. 11.25, 26 #
Mphu. 28.1-5
“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. 15Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
Za kusala zakudya
16“Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. 17#Yud. 10.3Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu, 18kuti anthu asadziŵe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziŵe. Ndipo Atate akowo amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho.
Za chuma chakumwamba
(Lk. 12.33-34)
19 #
Yak. 5.2, 3 “Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. 20#Mphu. 29.11Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. 21Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
Maso ndiwo nyale za thupi
(Lk. 11.34-36)
22“Maso ndiwo nyale zounikira thupi la munthu. Ngati maso ako ali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala kuŵala. 23Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima. Tsono ngati kuŵala kumene kuli mwa iwe kusanduka mdima, mdima wakewo ndi wochita kuti goo!
Za Mulungu ndi Chuma
(Lk. 16.13; 12.22-31)
24“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.
25“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? 26Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame? 27Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake?
28“Ndipo mumaderanji nkhaŵa ndi zovala? Onani maluŵa akuthengo m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. 29#1Maf. 10.4-7; 2Mbi. 9.3-6 Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa. 30Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
31“Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’ 32Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi. 33Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso. 34Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
اکنون انتخاب شده:
Mt. 6: BLY-DC
هایلایت
کپی
مقایسه
به اشتراک گذاشتن
می خواهید نکات برجسته خود را در همه دستگاه های خود ذخیره کنید؟ برای ورودثبت نام کنید یا اگر ثبت نام کرده اید وارد شوید
Bible Society of Malawi