Lk. 5
5
Yesu aitana ophunzira ake oyamba
(Mt. 4.18-22; Mk. 1.16-20)
1 #
Mt. 13.1, 2; Mk. 3.9, 10; 4.1 Tsiku lina Yesu adaaimirira pamphepete pa nyanja ya Genesarete,#5.1: Nyanja ya Genesarete: Limeneli ndi dzina lina la nyanja ya Galileya. anthu ambirimbiri nkumamupanikiza kuti amve mau a Mulungu. 2Iye adaona zombo ziŵiri pamphepetepo. Asodzi anali atatulukamo, ndipo ankatsuka makoka ao. 3Yesu adaloŵa m'chombo chimodzi, chimene chinali cha Simoni, nampempha kuti asunthire pang'ono ku nyanja. Adakhala pansi, ndipo ali m'chombo momwemo, adayamba kuŵaphunzitsa anthuwo.
4Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, “Sunthirani kozamako, muponye makoka anu kuti muphe nsomba.” 5#Yoh. 21.3Simoni adati, “Aphunzitsi, usiku wonsewu takhalira kugwira ntchito, osapha kanthu, koma chifukwa Inuyo mwatero, chabwino ndiponya makoka.” 6#Yoh. 21.6Tsono iwo adaponyadi makoka, napha nsomba zambirimbiri, kotero kuti makokawo ankayamba kung'ambika. 7Adachita kukodola anzao a m'chombo china chija kuti adzaŵathandize. Iwo adabwera, ndipo adadzaza zombo ziŵiri zonse zija mpaka zinali pafupi kumira.
8Pamene Simoni Petro adaona zimenezo, adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu nati, “Pepani Ambuye, mundichokere, ndine munthu wochimwa.” 9Adaatero popeza kuti iye, pamodzi ndi onse amene anali naye, adaazizwa nako kuchuluka kwa nsomba zimene adaaphazo. 10Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo, anzake a Simoni, nawonso adaazizwa. Tsono Yesu adauza Simoni kuti, “Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.” 11Motero, atakokera zombozo ku mtunda, adasiya zonse namatsata Yesu.
Yesu achiritsa munthu wakhate
(Mt. 8.1-4; Mk. 1.40-45)
12Pamene Yesu anali m'mudzi wina, kudabwera munthu wina wa khate thupi lonse. Pamene adaona Yesu, adadzigwetsa moŵerama pansi pamaso pake nayamba kumdandaulira. Adati, “Ambuye, mutafuna, mungathe kundichiritsa.” 13Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha. 14#Lev. 14.1-32 Tsono Yesu adamuuza kuti, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.” 15Komabe mbiri ya Yesu inkawandirawandira, ndipo makamu ambiri a anthu ankasonkhana kuti amve mau ake, ndiponso kuti aŵachize nthenda zao. 16Koma Iye adapita kumalo kosapitapita anthu, namakapemphera kumeneko.
Yesu achiritsa munthu wa ziwalo zakufa
(Mt. 9.1-8; Mk. 2.1-12)
17Tsiku lina Yesu ankaphunzitsa. Pomwepo padaakhala Afarisi ena ndi aphunzitsi ena a Malamulo, ochokera ku midzi yonse ya ku Galileya, ndi ya ku Yudeya, ndiponso ku Yerusalemu. Mphamvu zochokera kwa Ambuye zinali mwa Iye kuti azichizira odwala. 18Tsono kudafika anthu ena ndi munthu wofa ziwalo, atamnyamulira pa machira. Adayesa kuloŵa naye m'nyumba kuti amkhazike pamaso pa Yesu. 19Koma chifukwa anthu adaachuluka, sadapeze poloŵera naye. Motero adakwera pa denga, nachotsapo mapale ena, nkumutsitsa ndi machira ake omwe kumufikitsa pansi pakati pa anthu, pamaso pa Yesu. 20Poona chikhulupiriro chaocho, Yesu adati, “Mbale wanga, machimo ako akhululukidwa.”
21Apo aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi aja adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Ndaninso kodi amene akunyoza Mulungu mwachipongweyu? Ndani angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?” 22Yesu adaadziŵa maganizo ao, ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zimenezo mumtima mwanu? 23Chapafupi koposa nchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, yamba kuyenda?’ 24Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, ndikuti dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.” 25Pomwepo wodwalayo adadzukadi onse akupenya, ndipo adatenga machira aja amene adaagonapo, namapita kwao akutamanda Mulungu. 26Anthu onse aja adazizwa kwambiri, nayamba kutamanda Mulungu. Adagwidwa ndi mantha nati, “Taona zodabwitsa lero.”
Yesu aitana Levi
(Mt. 9.9-13; Mk. 2.13-17)
27Pambuyo pake Yesu adatuluka naona munthu wokhometsa msonkho, dzina lake Levi, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” 28Iye adanyamuka, nasiya zonse, nkumamutsatadi.
29Tsono Levi adamkonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake. Okhometsa msonkho ambirimbiri, pamodzi ndi anthu ena, anali nao paphwandopo. 30#Lk. 15.1, 2Afarisi pamodzi ndi aphunzitsi ao a Malamulo adayamba kuŵinya, nafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji mukudya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa?” 31Yesu adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala. 32Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa, kuti atembenuke mtima.”
Za kusala zakudya
(Mt. 9.14-17; Mk. 2.18-22)
33Anthu ena adauza Yesu kuti, “Ophunzira a Yohane amasala zakudya kaŵirikaŵiri nkumapemphera, chimodzimodzinso ophunzira a Afarisi. Koma ophunzira anu amangodya ndi kumwa.” 34Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! 35Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.”
36Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Munthu sang'amba chigamba ku chovala chatsopano nkuchisokerera pa chovala chakale. Chifukwa akatero, waononga chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chatsopanocho sichidzayenerana ndi chovala chakale chija.
37“Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale.#5.37: m'matumba achikopa akale: Pa nthaŵi imeneyo m'dziko la Palestina ankathira vinyo m'matumba achikopa. Matumba atsopano amatukumuka bwino akathiramo vinyo, koma akale amaphulika msanga. Chifukwa akatero, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba aja. Choncho vinyoyo adzatayika, matumbawo nkutha ntchito. 38Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.
39“Ndipo munthu akangolaŵa vinyo wakale, watsopano sangamufune. Pajatu amati, ‘Wakale ndiye vinyo chaiye.’ ”
اکنون انتخاب شده:
Lk. 5: BLY-DC
هایلایت
کپی
مقایسه
به اشتراک گذاشتن
می خواهید نکات برجسته خود را در همه دستگاه های خود ذخیره کنید؟ برای ورودثبت نام کنید یا اگر ثبت نام کرده اید وارد شوید
Bible Society of Malawi