1
Mk. 4:39-40
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Yesu adadzuka, ndipo adadzudzula mphepoyo, nalamula nyanja kuti, “Tonthola! Khala bata!” Mphepo ija idalekadi, kenaka padagwa bata lalikulu. Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha? Kani mulibe chikhulupiriro inu?”
مقایسه
Mk. 4:39-40 را جستجو کنید
2
Mk. 4:41
Koma iwo adaagwidwa ndi mantha kwambiri, nkumafunsana kuti, “Kodi Iyeyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?”
Mk. 4:41 را جستجو کنید
3
Mk. 4:38
Koma nthaŵi imeneyo Yesu anali kumbuyo m'chombomo, ali m'tulo atatsamira mtsamiro. Pamenepo ophunzira aja adamudzutsa, adati, “Aphunzitsi, kodi simukusamalako kuti tikumira?”
Mk. 4:38 را جستجو کنید
4
Mk. 4:24
Adaŵauzanso kuti, “Muzisamala pa mau amene mumamva. Muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu, ndipo inuyo adzakubzoletserani.
Mk. 4:24 را جستجو کنید
5
Mk. 4:26-27
Yesu adaŵauzanso kuti, “Za Ufumu wa Mulungu tingazifanizire motere: munthu afesa mbeu m'munda. Iyeyo atha kumangogona usiku, m'maŵa nadzuka, nthaŵi yonseyo mbeu adafesa zija zikumera ndi kukula, mwiniwakeyo osadziŵa m'mene zonsezi zikuchitikira.
Mk. 4:26-27 را جستجو کنید
6
Mk. 4:23
Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!”
Mk. 4:23 را جستجو کنید