1
MACHITIDWE 16:31
Buku Lopatulika
BLP-2018
Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.
مقایسه
MACHITIDWE 16:31 را جستجو کنید
2
MACHITIDWE 16:25-26
Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva; ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.
MACHITIDWE 16:25-26 را جستجو کنید
3
MACHITIDWE 16:30
nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?
MACHITIDWE 16:30 را جستجو کنید
4
MACHITIDWE 16:27-28
Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa. Koma Paulo anafuula ndi mau aakulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno.
MACHITIDWE 16:27-28 را جستجو کنید