Matayo 28
28
Kuhyuka kwa Yesu
Maluko 16:1-10; Luka 24:1-12; Yohana 20:1-10
1Siku Lopumulila yapo lidata, umawamawa siku la juma pili Maliya wa ku Magidala ni Maliya mwina yujha adapita kupenya pa chiliza. 2Kwa chizulumukila, kudali chimtingiza chachikulu, mtumiki wa kumwamba wa Amnungu wadachika kuchokela kumwamba adapita kuchiliza ni kuugadabula mwala ujha ni kuukhalila. 3Mtumiki wa kumwamba yujha wamang'azikila ngati mbhambe, ni njhalu zake zidali zoyela mbee. 4Alonda wajha adaopa kupunda, amatendhemela ni adaoneka ngati amwalila.
5Mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadaakambila wachikazi wajha, “Msadaopa! Nijhiwa kuti mumfunafuna Yesu uyo wadapachikidwa pamtanda. 6Palibemo muno, wathohyuka ngati mujha iye wadakambila. Majhani mpenye malo yayo adamuika. 7Pitani msanga mkaakambile woyaluzidwa wake kuti, ‘Yesu wahyuka, nayo wakuchogolelani kupita ku Galilaya, kumeneko nde uko simkamuone!’ Kumbukilani icho nakukambilani.”
8Chimwecho waachikazi wajha adachoka pachiliza uku niaopa ni kukondwela, adathamanga kupita kwaakambila oyaluzidwa wake nghani zimenezo.
9Pampajha, Yesu wadapezana nao, wadaakambila, “Moni!” Waachikazi wajha adamsendelela ni kumgwila myendo yake, adamlambila. 10Ndiipo Yesu wadaakambila, “Musadaopa! Pitani mkaakambile acha abale wanga apite ku Galilaya, ndeuko siakanione.”
Alonda akamba icho chidachokela
11Wachikazi yapo adali mnjila, alonda akumojhi yawo amalonda chiliza adabwela ku mujhi ni kwaakambila wakulu wa ajhukulu vindhu vonjhe ivo vidachokela. 12Ajhuku wa akulu adakomana ni akulu adavomelezana chindhu, adaapacha alonda wajha ndalama zambili, 13adaakambila, “Kambani, ‘Oyaluzidwa wake adajha usiku kuba chitanda chake ife yapo tidagona.’ 14Nghani izi zikamfikila mlamuli, ife sitikambe naye nianyiimwe simlowa mavuto.”
15Alonda adalandila ndalama ni adachita ngati mujha adakambilidwa. Mbili iyi idaenela kwa Ayahudi mbakana lelo.
Yesu waatulukila oyaluzidwa wake
Maluko 16:14-18; Luka 24:36-49; Yohana 20:19-23; Vichito 1:6-8
16Ndiipo oyaluzidwa khumi ni mmojhi adapita ku Galilaya, kuphili uko Yesu wadaakambila apite. 17Yapo adamuona Yesu, adamlambila, uku wina ni amukhaikila. 18Yesu wadajha pafupi pao ni kwaakambila, “Napachidwa ulamulilo wa kuchogoza kumwamba ni jhiko lapanjhi. 19Chipano pitani kwa wandhu maiko yonjhe, mkaachite kukhala oyaluzidwa, mkaabatize kwa jhina la Atate ni la Mwana ni la Mzimu Woyela, 20ni mwaayaluze kuyagwila yonjhe yayo nakulamulilani. Zenedi, ine nili pamojhi namwe muyaya mbaka mathelo ya jhiko la panjhi.”
Currently Selected:
Matayo 28: NTNYBL2025
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: