YouVersion Logo
Search Icon

Maluko 1

1
Yohana Mbatizi waalalikila wandhu
Matayo 3:1-12; Luka 3:1-18; Yohana 1:19-28
1Uwu ni Uthenga Wabwino uwo umuusu Yesu Kilisito, Mwana wa Mnungu. 2Udayamba ngati umo udalembedwa ni mlosi Isaya,
“Mnungu wadakamba, ‘Sinimtume mthenga wanga wakuchogolele,
uyo siwaikonje njila yako.’
3Mundhu watana kuchokela kuphululu,
‘Ikonjeni njila ya Ambuye,
mjhikonje kwalandila Ambuye yapo siajhe!’”
4Chimwecho, mthenga mmeneyo wadali Yohana Mbatizi, wadachokela kuphululu, niwaalalikila wandhu ni kwaabatiza, niwakamba, “Lapani machimo yanu ni kuti mubatizidwe, ni Mnungu siwakulekeleleni machimo yanu.” 5Wandhu ambili amachokela ku jhiko la Yudea ni mmujhi wa Yelusalemu, amapita kumvechela Yohana. Amalapa machimo yao, niiye wamaabatiza mumchinjhe Yolodani.
6Yohana wadavala chiwalo chidakonjedwa ni mabweya ya chinyama icho chimatanidwa ngamiya, ni lamba la chikwetu mchiuno mwake. Chakudya chake chidali nzige ni uchi wa kuthengo. 7Yohana wadauzila wandhu, “Mmbuyo mwanga wakujha mundhu uyo wali wamkulu kupitilila ine. Ine sinifunika ata kumasula vingwe va malapasi yake. 8Ine nikubatizani kwa majhi, nambho iye siwakubatizeni kwa Mzimu Woyela.”
Yesu wabatizidwa ni kuyesedwa
Matayo 3:13; 4:11; Luka 3:21-22; 4:1-14
9Ndhawi imeneyo Yesu wadachokela mmujhi wa Nazaleti, mujhiko la Galilaya, wadafika kwa Yohana, nayo wadambatiza mumchinje Yolodani. 10Yesu yapo wadachuuka mmajhi, pamwepo wadaona kumwamba kwamasulidwa, ni Mzimu Woyela udamchikila ngati nghunda. 11Mvekelo wa Mnungu udaveka kuchokela kumwamba, niukamba, “Iwe nde mwana wanga uyo nikukonda, nikondelechedwa ni iwe.”
12Pampajha, Mzimu Woyela udamchogoza Yesu kupita kuphululu, 13wadakhala kumeneko masiku alobaini, niwaesedwa ni Satana. Ni zinyama zamthengo zidali kumeneko, ni atumiki akumwamba a Mnungu adamtumikila.
Yesu waatana alovi anayi amchate
Matayo 4:12-22; Luka 4:14-15; 5:1-11
14Pambuyo pa masiku yambili, Yohana wadamangidwa mndende. Yapo wadali mndende, Yesu wadapita ku Galilaya, wadaalalikila wandhu Uthenga Wabwino wa Mnungu. 15Wadakamba, “Nyengo ya Mnungu yakwana yolamulila wandhu. Lapani ni kukhulupilila Uthenga Wabwino.” 16Siku limojhi Yesu wamayenda mmbhepete mwanyanja ya Galilaya, wadaaona alovi awili, Simoni ni mphwake Andulea, amatovuwa njhomba. 17Yesu wadaakambila, “Nichateni, nane sinikuyaluzeni mukhale owapeleka wandhu kwa ine, ngati umo mmavuwila njhomba.” 18Pampajha adavisia vilepa vao nikumchata. 19Wadapita pachogolo pang'ono, wadaaona Yakobo ni Yohana, wana a Zebedayo. Adakhala mbwato wao, amatotambasula vilepa vawo. 20Pampajha Yesu yapo wadaona, wadaatana. Anyiiwo adaasiya atate wao a Zebedayo mbwato pamojhi ni wopota njhito wina, adamchata Yesu.
Yesu wamlamicha mundhu wa chiwanda
Luka 4:31-37
21Pambuyo, Yesu ni woyaluzidwa wake adafika mmujhi wa Kapelenaumu. Siku Lopumulila, Yesu wadalowa mnyumba iyo akomanilana Ayahudi, wadayamba kwayaluza wandhu. 22Wandhu yawo adamvela mayaluzo yake, adazizwa ndande siwamayaluze ngati umo amayaluzila oyaluza athauko la Musa, nambho iye wamayaluza ngati mundhu wa ulamulilo. 23Pampajha wadatulukila mundhu wachiwanda mujha mnyumba yokomanilana Ayahudi, wadakweza mvekelo waukulu, 24“Ufuna kutichita chiyani iwe Yesu wa ku Nazaleti? Bwanji, wajha kutipha? Ine nijhiwa kuti iwe ni Woyela, kuchokela kwa Mnungu!” 25Yesu wadachinyindila chiwanda, “Khala chete! Mchoke mundhu uyu.” 26Chiwanda chimenecho chidamtingiza kwa mbhavu mundhu yujha, chidalila kwa mvekelo waukulu, ni kumchoka. 27Wandhu wonjhe adazizwa kupunda ni kufunjhana, “Vindhu vanji ivi? Yaya ni mayaluzo ya chipano! Mundhu uyu wali ni ulamulilo wochocha viwanda, navo vimuvela!” 28Chimwecho, nghani za Yesu zidayenela chisanga mmalo monjhe mwa jhiko la Galilaya.
Yesu waalamicha wandhu ambili
Matayo 8:14-17; Luka 4:38-41
29Yesu ni oyaluzidwa wake Simoni, ni Anduleya ni Yakobo ni Yohana, adachoka Mnyumba yokomanilana Ayahudi, adapita kukhomo kwa Simoni ni mphwake Anduleya. 30Apongozi wake waakazi a Simoni, adali agona pachika niadwala homa. Yesu yapo wadafika, adamkambila nghani za wodwala mmeneyo. 31Yesu wadaasendelela wajhja maye, nikwaagwila jhanja, wadaanyakula. Ni homa idamchoka, wadayamba kwatumikila.
32Ujhulo yapo udafika, Siku Lopumulila yapo lidatha, wandhu adampelekela Yesu odwala onjhe ni anyiawo adali ni viwanda. 33Wandhu ambili ammujhi ujha adakomana pa liwala la nyumba. 34Yesu wadaalamicha wandhu ambili yawo adali ni matenda yosiyana siyana, ni wadavitopola viwanda vambili. Siwadavilole viwanda vikambe, pakuti vimamjhiwa kuti iye ni yani.
Yesu waalalikila wandhu ku jhiko la Galilaya
Luka 4:42-44
35Umawamawa siku lidachatila, Yesu wadapita kubwalo kwa mujhi, pamalo yapo padalibe wandhu, kumeneko wadampembha Mnungu. 36Simoni ni achanjake adapita kumfunafuna. 37Yapo adamuona, adamkambila, “Wandhu wonjhe atokufunafuna iwe.” 38Yesu wadaakambila, “Tiyeni ku vijhijhi vina va pafupi. Mmenemo nifunika naalalikile wandhu Uthenga wa Bwino, ndande chimenecho nde icho nachijhela.” 39Chimwecho, Yesu wadapita mmalo yonjhe ya ku jhiko la Galilaya niwaalalikila wandhu mnyumba yokomanilana Ayahudi ni kutopola viwanda.
Yesu wamulamicha mundhu makate
Matayo 8:1-4; Luka 5:12-16
40Mundhu mmojhi uyo wadali ni makate wadampitila Yesu, wadamgwadila wadampembha, wadakamba, “Ukafuna ukhoza kuniyelecha, kuti nikhoze kumlambila Mnungu!” 41Yesu wadamlengela lisungu mundhu mmeneyo, wadatambasula jhanja lake ni wadamgafya, kumkambila, “Nifuna, uyelechedwe!” 42Pampajha makate yadamchoka mundhu mmeneyo, nayo wadalama. 43Pampajha, Yesu wadamkambila wapite, uku niwamuonya ni wadamkambila, 44“Siudamkambila mundhu waliyonjhe chindhu ichi, nambho pita ukajhilangize kwa ajhukulu a Mnungu ni ukachoche njhembe ngati umo wadalamulila Musa ni ujhilangize kwa wandhu kuti walama.” 45Nambho mundhu mmeneyo siwadasiye kuuzila nghani zimenezo mmalo yonjhe. Chimwecho Yesu siwadakoze kulowa mmujhi waliwonjhe padanga. Chimwecho Yesu wadakhala pamalo popande wandhu, nambho wandhu amampitila kuchokela kila kumalo.

Currently Selected:

Maluko 1: NTNYBL2025

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in