Matayo 27
27
Yesu wapelekedwa kwa Pilato
Maluko 15:1; Luka 23:1-2; Yohana 18:28-32
1Umawamawa, wakulu wa ajhukulu onjhe ni akulu a wandhu adavomelezana kumupha Yesu. 2Adammanga vingwe ni kumpeleka kwa Pilato, uyo wadali Mloma.
Yuda wajhimangila
Vichito 1:18-19
3Yuda, uyo wadamng'anamuka Yesu, yapo wadaona kuti Yesu walamlidwa kuphedwa, wadandaula ni wadabweza vijha vibandhu selasini va madini ivo vitanidwa ndalama izo wadatenga kwa achogoleli a ajhukulu ni akulu a wandhu. 4Wadaakambila, “Nalwakwa, pakuti namng'anamuka mundhu wosalakwa kuti waphedwe!”
Anyiiwo adamuyangha, “Ife tilibemo, zako umwene!”
5Yuda wadazitaya ndalama zimenezo mnyumba ya Mnungu, ndiipo wadachoka ni kupita kujhimangila chingwe mkhosi.
6Waakulu wa ajhukulu adatondola gelejha za ndalama zijha ni kukamba, “Iyi ni ndalama ya mwazi, siiloledwa kusingizana ni njhembe za Mnyumba ya Mnungu.” 7Chimwecho, yapo adamaliza kuvomelezana, adalamula kuzitumila kugulila munda wa oumba mbiya, kuti pakhale malo yozikila alendo. 8Iyi ndendande munda ujha utanidwa Munda wa Mwazi mbaka lelo.
9Chimwecho mawu yajha wadakamba mlosi Yelemiya lakwanila, “Siatenge vibandhu selasini za ndalama izo wandhu a ku Izilaeli adavomelezana kulipa ndande ya iye, 10adatumila ndalamazo kugulila Munda wa oumba, ngati umo wadaagiza Ambuye.”
Yesu pachogholo pa Pilato
Maluko 15:2-5; Luka 23:3-5; Yohana 18:33-38
11Yesu wadaima pachogolo pa wamkulu wa ku Loma, wamkulu mmeneyo wadamfunjha, “Bwanji, iwe nde mfumu wa Ayahudi?”
Yesu wadayangha, “Iwe ukamba.” 12Nambho wakulu a ajhulu ni wakulu adampacha mlandu, Yesu siwadayanghe chindhu.
13Ndiipo Pilato wadamfunjha Yesu, “Bwanji siuvela milandhu iyi achocha kwaiwe?”
14Nambho Yesu siwadayanghe ata mau limoji, ni wamkulu mmeneyo wadazizwa kupunda.
Yesu walamulidwa kuphedwa
Maluko 15:6-15; Luka 23:13-25; Yohana 18:39; 19:16
15Kila pwando la Pasaka, wamkulu wa ku Loma wadali ni chikalidwe cha kummasulila mundhu mmojhi wa mndende uyo wamafunika ni wandhu. 16Ndhawi imeneyo kudali womangidwa mmojhi wadajhiwika kupunda, wamatanidwa Balaba. 17Wandhu yapo adapezana pamoji, Pilato wadaafunjha, “Mfuna ni mmasulile yani? Bwanji nimmasulile balaba kapina Yesu watanidwa Kilisito?” 18Pilato wadakamba chimwecho ndande wadajhiwa kuti Ayahudi adampeleka yesu kwake ndande amamuonela njhanje.
19Pilato yapo wadakhala pampando wa malamulo, mkazake wadampelekela utengha uwo umakamba, “Usamchita chalichonjhe uyu mundhu siwadalakwe, ndande usiku wa lelo nachauchika kupunda mumaloto chifuko cha iye.”
20Nambho wakulu wa ajhukulu ni waakulu a wandhu adalikhwilizila gulu la wandhu limpembhe Pilato wamasulule Balaba ni Yesu waphedwe. 21Pilato wadaafunjhanjho, “Pakati pa anyiyawa awili, yuti mufuna ni mmasule?”
Adayangha, “Balaba!”
22Pilato wadafunjha, “Nimchite chiyani uyu Yesu watanidwa Kilisito?”
Onjhe adakamba “Wapachikidwe pamtanda!”
23Pilato wadaafunjha, “Ndande yanji? Wachita chindhu chanji choipa?”
Adamkambila “Mpachikeni pamtanda!”
24Pilato yapo wadajhiwa kuti siwakoza kuchita chalichonjhe, ni mkangajhili umatoyamba, wadatenga majhi ni kusamba mmanja, pamaso pa gulu ni wadakamba, “Ine nilibemo pa nyifa ya mundhu uyu, izo zanu mwachina wene!”
25Wandhu wonjhe adayangha, “Kulakwa kumeneko kwa kumpha Yesu sikukhale kwaife ni wana watu!”
26Ndiipo wadammasulila Balaba ni adalamula Yesu wabulidwe mikwapulo, wadapacha kuti akampachike pamtanda.
Asikali amchitila chipongwe Yesu
Maluko 15:16-20; Yohana 19:2-3
27Ndiipo asikali a Pilato adampeleka Yesu kuseli kwa nyumba ya mfumu, ndiipo gulu lonjhe la asikali lidamzungulila. 28Adamvula njhalu zake ni kumveka njhalu ya chifumu. 29Adasoka nghata ya minga nikumveka kumutu, adamwikila mkwapulo kujanja lake la kwene. Adagwada pachogolo pake ni kumchitila vipongwe uku niakamba, “Moni mfumu wa Ayahudi!” 30Adamlavulila malovu, adaitenga ijha mkwapulo ni kumbula nawo kumutu. 31Yapo adamaliza kumchitila chipongwe, adamvula njhalu ijha ya chifumu ni kumveka njhalu zake. Ndiipo adampeleka wakapachikidwe pamtanda.
Yesu wapachikidwa pamtanda
Maluko 15:21-32; Luka 23:26-43; Yohana 19:17-27
32Yapo amachoka, adamkomana ni wammuna wakusilia jina lake Simoni adamkakamiza waubale mtanda wa Yesu. 33Adapita pamalo patanidwa Goligota mateyake, malo ya Chifuvu cha Mutu. 34Adampacha divai yali ni ndulu wamwe nambho yapo wadailawa wadakana kuimwa.
35Adampachika pamtanda ni kugawana njhalu, zake kwa kuzibulila ghudughudu.
36Adakhala pamwepo kumchita ulonda. 37Chibao chidali pamwamba pa mtanda wake chidalembedwa chimwechi, “Uyu ni Yesu, Mfumu wa Ayahudi.” 38Anghunghu awili nawo adapachikidwa pamojhi ni Yesu kila mmojhi wadali ni mtanda wake mmojhi kwene ni mwina kumanjele kwake.
39Wandhu amapita pamenepo, adatingiza mitu yao ni kumtukwana Yesu. 40Niakamba, “Iwe! Siudajhidama kuti siuligomole nyumba ya Mnungu ni kuimanga kwa siku zitatu? Chipano jhilamiche umwene. Ngati iwe ni Mwana wa Mnungu, chika pamtanda!”
41Chimchijha wakulu wa ajhukulu ni oyaluza thauko ni waakulu adamchita chipongwe. 42Adakamba, “Wadalamicha wandhu wina walepela kujilamicha mwene wake! Iye ngati mfumu wa Izilaeli wachike chipano pamtanda, ife sitimkulupilile! 43Wadamkhulupilila Mnungu wadakamba kuti iye ni mwana wa Mnungu. Chipano tiyeni tione ngati Mnungu siwamuombole.”
44Chimchijha wajha anghunghu awili wadapachikidwa pamojhi niiye, adamtukwana.
Kufa kwa Yesu pamtanda
Maluko 15:33-41; Luka 23:44-49; Yohana 19:28-30
45Kuchokela saa sita mbaka sa tisa usana, mdima udavinikila jhiko lonjhe. 46Yapo idafika saa tisa, Yesu wadakweza mvekelo, “Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Mate yake, “Mnungu wanga, Mnungu wanga, mbona mwanisiya?”
47Wandhu adaima pajha yapo adavela, adakamba, “Wamtana Eliya!” 48Kankamojhi, mmojhi wao wadathamanga, wadatenga buula ni kubiza mu divai yowawa, ni wadaika panjhonga pa mkwapulo ni kumapacha Yesu kuti wafifinye.
49Nambho wina adakamba, “Msiyeni, tione ngati Eliya siwajhe kumuombola.”
50Yesu wadatananjho kwa mvekelo waukulu, wadamwalila.
51Pampajh, panzia ilo lidapachikidwa mnyumba ya Mnungu, lidang'ambika pakati kuyambila kumwamba mbaka panjhi. Jhiko lidatingizika ni ndhaka idasweka, 52viliza vidamasuka, ni wandhu ambili a Mnungu yawo adamwalila, adahyuka. 53Yesu yapo wadahyuka wandhu ambili adachoka mmanda, adalowa ku Yelusalemu mu Mujhi Woyela, wandhu ambili wadaaona.
54Yujha wamkulu wa asikali, pamojhi ni asikali yawo amalonda chiliza cha Yesu, yapo adaona chimtingiza cha ndhaka ni kila kandhu yako kadachitika, adagwilidwa ni mandha, adakamba, “Zenedi, uyu wadali Mwana wa Mnungu!”
55Pameneko adalipo waachikazi ambili yawo amapenyecha kwa patali, nde yawo adamchata Yesu kutoka ku Galilaya ni amtumikila iye. 56Pakati pa wachikazi achameneo adalipo Malia wa kumujhi wa Magidala ni Maliya maye wao wang'ono wachi Yakobo ni Yusufu, pamojhi ni mkazi wa Zebedayo.
Yesu wazikidwa
Maluko 15:42-47; Luka 23:50-56; Yohana 19:38-42
57Ujhulo yapo udajha, wadajha wopata mmojhi kuchokela ku Alimataya, jhina lake Yusufu, Mundu mmeneyo nayo wadali mmojhi wa oyaluzidwa a Yesu. 58Wadampitila Pilato, wadawenda kuti wapachidwe chitanda cha Yesu. Pilato wadalamula kuti wapachidwe. 59Ndiipo Yusufu wadatenga chitanda cha Yesu ni kuchiveka sanda, 60wadachiika chitanda muchiliza chake cha chipano icho wadakumba mundhaka yolimba. Ndiipo wadauvilingicha mwala waukulu pakhomo la chiliza ni kuchokapo. 61Maliya wa ku Magedala ni Maliya mwina yujha adakhala niapenyechana ni chilizacho.
Asikali alonda chiliza cha Yesu
62Siku ilo lidachata lidali siku lo Lopumula, ajhukulu wa mkulu ni Afalisayo adampitila Pilato, 63adamkambila, “Imwe ambuye, tikumbukila yujha mundhu wamthila, yapo wadali wakali wa moyo, wadakamba, ‘Sinihyuke siku la katatu.’ 64Chimwecho lamulani kuti chiliza chilondedwe kwa masiku yatatu. Popande chimwecho oyaluzidwawake akhoza kujha ni kuba thupi lake ni kwakambila wandhu wahyuka. Unami umenewo wothela siukhale woipa kupunda kusiyana ni ujha woyamba.”
65Pilato wadakamba, “Mulinao alonda, pitani mkalonde chiliza ngati umo mukhozela.”
66Chimwecho adapita ku chiliza pamojhi ni alonda pakuika chidindo pa mwala ni kwaasiya asikali alilonde.
Currently Selected:
Matayo 27: NTNYBL2025
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: