YouVersion Logo
Search Icon

AFILIPI 3

3
Awachenjeza asatsate atumwi onyenga. Aonetsere zipatso za Mzimu
1 # 1Ate. 5.16 Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa. 2#Agal. 5.15Penyererani agalu, penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula; 3#Yoh. 4.23-24pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi; 4#2Ako. 11.18, 21ndingakhale inenso ndili nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu; 5#Gen. 17.12; 2Ako. 11.22wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi; 6#Mac. 9.1; Aro. 10.5monga mwa changu, wolondalonda Mpingo; monga mwa chilungamo cha m'lamulo wokhala wosalakwa ine. 7#Mat. 13.44Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Khristu. 8Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu, 9#Aro. 3.21-22ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro; 10#Aro. 6.3-5kuti ndimzindikire Iye, ndi mphamvu ya kuuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake; 11ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa. 12#1Tim. 6.12Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu. 13#Luk. 9.62; 1Ako. 9.24, 26Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo, 14#2Tim. 4.7-8ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu. 15#1Ako. 14.20Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu; 16#Agal. 6.15-16chokhachi, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.
17 # 1Ako. 4.16 Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu. 18#Agal. 6.12Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu; 19#2Ako. 11.15; Aro. 8.5; 16.18chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko. 20#Mac. 1.11; Akol. 3.1, 3Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu; 21#1Ako. 15.43, 48-49amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.

Currently Selected:

AFILIPI 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in