YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 52

52
1 # Yes. 51.9, 17; Nah. 1.15 Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako, Ziyoni; tavala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa. 2Dzisanse fumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam'nsinga wa Ziyoni.
3 # Mas. 44.12 Pakuti atero Yehova, Inu munagulitsidwa chabe, ndipo mudzaomboledwa opanda ndalama. 4#Gen. 46.6; Mac. 7.14-15Pakuti Ambuye Yehova atero, Anthu anga ananka ku Ejipito poyamba paja, kukakhala kumeneko; ndipo Asiriya anawatsendereza popanda chifukwa. 5#Ezk. 36.20, 23; Aro. 2.24Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza. 6Chifukwa chake anthu anga adzadziwa dzina langa; chifukwa chake tsiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano.
7 # Nah. 1.15 Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu. 8Mau a alonda ako! Akweza mau, aimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni. 9#Yes. 48.20; 51.3Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu. 10#Mas. 98.1-3; Mat. 26.63; 27.12, 14Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu. 11#Lev. 22.1-33; Yer. 51.6, 45; 2Ako. 6.17Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova. 12#Eks. 14.19Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.
13 # Yer. 23.5; Afi. 2.9 Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba. 14#Mas. 22.6-7; Yes. 53.2-3Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israele, momwemo nkhope yake yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu aliyense, ndi maonekedwe ake kupambana ana a anthu; 15#Ezk. 36.25; Aro. 15.21; Aheb. 9.13-14momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwa kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.

Currently Selected:

YESAYA 52: BLPB2014

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in