YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 51

51
Israele akonzedwanso napulumutsidwa
1 # Aro. 9.30-32; Gen. 12.1-2; 24.1, 35 Mverani Ine, inu amene mutsata chilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani kuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo. 2#Aro. 4.1, 16Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumchulukitsa. 3#Gen. 2.8; Yes. 52.9Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi nkhwangwara yake ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.
4Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzachokera kwa Ine, ndipo ndidzakhazikitsa chiweruziro changa chikhale kuunika kwa anthu. 5#Aro. 1.16-17Chilungamo changa chili pafupi, chipulumutso changa chamuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga. 6#Mas. 102.27-28; Yes. 50.9; Mat. 24.35Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.
7 # Mas. 37.31; Mat. 10.28 Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao. 8#Yes. 50.9Pakuti njenjete idzawadya ngati chofunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma chilungamo changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chipulumutso changa kumibadwo yonse.
9 # Mas. 44.1; Yes. 52.1 Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija? 10#Eks. 14.21Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa? 11#Yes. 35.10Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.
12 # Yes. 51.3; 1Pet. 1.24 Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu; 13#Yes. 40.22waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse chifukwa cha ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? Uli kuti ukali wa wotsendereza? 14Wam'nsinga wowerama adzamasulidwa posachedwa; sadzafa ndi kutsikira kudzenje, chakudya chake sichidzasowa. 15#Yer. 31.35Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ake akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lake. 16#Deut. 18.18; Yes. 49.2Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.
Agalamuke Yerusalemu
17 # Yer. 25.15-16 Galamuka, galamuka, imirira Yerusalemu amene unamwa m'dzanja la Yehova chikho cha ukali wake; iwe wamwa mbale ya chikho chonjenjemeretsa ndi kuchigugudiza. 18Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana amuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera. 19Izi ziwiri zakugwera; ndani adzakulira iwe? Bwinja ndi chipasuko, njala ndi lupanga; ndidzatonthoza mtima wako bwanji? 20Ana ako amuna akomoka; agona pamtu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako. 21#Mali. 3.15Chifukwa chake imva ichi tsopano, iwe wovutidwa ndi woledzera koma si ndi vinyo ai; 22#Yer. 50.34atero Ambuye ako Yehova, ndi Mulungu wako amene anena mlandu wa anthu ake, Taona, ndachotsa m'dzanja mwako chikho chonjenjemeretsa, ngakhale mbale ya chikho cha ukali wanga; iwe sudzamwa icho kawirinso. 23#Mas. 66.11-12; Zek. 12.2Ndidzachiika m'dzanja la iwo amene avutitsa iwe; amene anena kumoyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.

Currently Selected:

YESAYA 51: BLPB2014

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in