YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 26

26
Nyimbo yakulemekeza kutchinjiriza kwa Yehova
1 # Yes. 60.18 Tsiku limenelo adzaimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tili ndi mudzi wolimba; Iye adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga. 2#Mas. 118.19-20Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene uchita zoonadi, ulowemo. 3#Yes. 30.15Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu. 4#Deut. 32.4Khulupirirani Yehova nthawi yamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire. 5#2Maf. 19.28Chifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa fumbi. 6Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphawi, ndi mapondedwe a osowa. 7#Mas. 37.23Njira ya wolungama ili njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama. 8#Yes. 64.5Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu. 9#Mas. 63.6Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo. 10#Aro. 2.4-5Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.
11Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu. 12#Mik. 5.4-5Yehova, mudzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira ntchito zathu zonse. 13Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu Ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzatchula dzina lanu. 14Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; chifukwa chake Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa chikumbukiro chao chonse. 15Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.
16 # Hos. 5.15 Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga. 17#Yoh. 16.21Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yake yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kufuula m'zowawa zake; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova. 18Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinachite chipulumutso chilichonse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe. 19#Ezk. 37; Dan. 12.2Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.
20 # Eks. 12.22-23 Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita. 21#Mik. 1.3; Yud. 14Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.

Currently Selected:

YESAYA 26: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in