YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 12

12
Chiyamiko cha anthu a Mulungu atalangidwa
1Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga. 2#Mas. 118.14Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa. 3#Yoh. 7.37-38Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso. 4#Mas. 148.13; Yoh. 17.1, 4, 6, 26Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. 5#Eks. 15.1Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse. 6Tafuula, takuwa iwe, wokhala m'Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.

Currently Selected:

YESAYA 12: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in