YouVersion Logo
Search Icon

HOSEYA 13

13
Tchimo la Israele ndi kulangidwa kwake
1 # 2Maf. 17.16, 18 Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza m'Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa. 2#1Maf. 19.18; Hos. 8.4Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe. 3#Mas. 1.4; Hos. 6.4Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame asansuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira. 4#Eks. 20.2; Yes. 43.11Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi. 5#Deut. 2.7Ndinakudziwa m'chipululu, m'dziko lotentha kwambiri. 6#Deut. 8.12, 14Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; chifukwa chake anandiiwala Ine. 7Chifukwa chake ndikhala nao ngati mkango; ngati nyalugwe ndidzalalira kunjira. 8#2Sam. 17.8Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula. 9#Deut. 33.26Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako. 10#1Sam. 8.5, 19Ili kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'midzi yako yonse? Ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga? 11#1Sam. 8.7; 16.1Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamchotsanso m'ukali wanga. 12Mphulupulu ya Efuremu yamangika, tchimo lake lisungika. 13Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asachedwe mobalira ana. 14#Yes. 25.8; 1Ako. 15.54-55Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga. 15#Yer. 4.11Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika. 16#2Maf. 15.16; 18.11-12Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.

Currently Selected:

HOSEYA 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in