YouVersion Logo
Search Icon

AEFESO 6

6
1 # Miy. 23.22; Akol. 3.20 Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. 2#Eks. 20.12Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), 3kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko. 4#Deut. 6.7, 20, 24; Akol. 3.21Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.
5 # Akol. 3.22-24 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwa Khristu; 6#Akol. 3.22-24si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima; 7#Akol. 3.22-24akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai; 8#Akol. 3.22-24podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu. 9#Aro. 2.11; Akol. 4.1Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye.
Zida za Mulungu
10 # Akol. 1.11 Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. 11#2Ako. 6.7Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. 12#Luk. 22.53; Aef. 2.2Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. 13#2Ako. 10.4Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. 14#Yes. 11.5; 59.17Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; 15#Yes. 52.7ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; 16#1Yoh. 5.4koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. 17#Yes. 59.17; Aheb. 4.12Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; 18#Akol. 4.2-4; 1Tim. 2.1mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, 19#Akol. 4.2-4; 2Ate. 3.1ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, 20#Akol. 4.2-4chifukwa cha umene ndili mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.
Tikiko apita naye kalatayo
21 # Akol. 4.7 Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; 22amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. 23#1Pet. 5.14Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. 24Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka.

Currently Selected:

AEFESO 6: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in