1
AEFESO 6:12
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
Compare
Explore AEFESO 6:12
2
AEFESO 6:18
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse
Explore AEFESO 6:18
3
AEFESO 6:11
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.
Explore AEFESO 6:11
4
AEFESO 6:13
Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.
Explore AEFESO 6:13
5
AEFESO 6:16-17
koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu
Explore AEFESO 6:16-17
6
AEFESO 6:14-15
Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere
Explore AEFESO 6:14-15
7
AEFESO 6:10
Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.
Explore AEFESO 6:10
8
AEFESO 6:2-3
Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.
Explore AEFESO 6:2-3
9
AEFESO 6:1
Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino.
Explore AEFESO 6:1
Home
Bible
Plans
Videos