1
Mk. 14:36
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Compare
Explore Mk. 14:36
2
Mk. 14:38
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Explore Mk. 14:38
3
Mk. 14:9
Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwino pa dziko lonse lapansi, azidzafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
Explore Mk. 14:9
4
Mk. 14:34
Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, koma mukhale masotu.”
Explore Mk. 14:34
5
Mk. 14:22
Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, ili ndi thupi langa.”
Explore Mk. 14:22
6
Mk. 14:23-24
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, naamwa onse. Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.
Explore Mk. 14:23-24
7
Mk. 14:27
Pambuyo pake Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa zidzangoti balala.’
Explore Mk. 14:27
8
Mk. 14:42
Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.”
Explore Mk. 14:42
9
Mk. 14:30
Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino usiku womwe uno, tambala asanalire kachiŵiri, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.”
Explore Mk. 14:30