Lk. 4:9-12
Lk. 4:9-12 BLY-DC
Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni.’ Ndiponso, “ ‘Iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ”





