Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo? Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lake, ndi kumphunzitsa Iye? Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya chiweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha?