YESAYA 40:6-7
YESAYA 40:6-7 BLPB2014
Mau a wina ati, Fuula. Ndipo ndinati, Kodi ndifuule chiyani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo; udzu unyala, duwa lifota; chifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu.





