1
Miyambo 29:25
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha, koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.
Compare
Explore Miyambo 29:25
2
Miyambo 29:18
Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo; koma wodala ndi amene amasunga malamulo.
Explore Miyambo 29:18
3
Miyambo 29:11
Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.
Explore Miyambo 29:11
4
Miyambo 29:15
Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.
Explore Miyambo 29:15
5
Miyambo 29:17
Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere ndi kusangalatsa mtima wako.
Explore Miyambo 29:17
6
Miyambo 29:23
Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.
Explore Miyambo 29:23
7
Miyambo 29:22
Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano, ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.
Explore Miyambo 29:22
8
Miyambo 29:20
Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.
Explore Miyambo 29:20