1
Miyambo 28:13
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.
Compare
Explore Miyambo 28:13
2
Miyambo 28:26
Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru, koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.
Explore Miyambo 28:26
3
Miyambo 28:1
Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa, koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.
Explore Miyambo 28:1
4
Miyambo 28:14
Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse, koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.
Explore Miyambo 28:14
5
Miyambo 28:27
Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.
Explore Miyambo 28:27
6
Miyambo 28:23
Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.
Explore Miyambo 28:23