1
Levitiko 19:18
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
“ ‘Musamubwezere mnzanu choyipa kapena kumusungira kanthu kunkhosi, koma konda mnansi wako monga iwe mwini. Ine ndine Yehova.
Compare
Explore Levitiko 19:18
2
Levitiko 19:28
“ ‘Musadzichekecheke pathupi panu chifukwa cha munthu wakufa kapena kudzitema mphini pa thupi lanu. Ine ndine Yehova.
Explore Levitiko 19:28
3
Levitiko 19:2
“Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Khalani oyera mtima chifukwa Ine, Yehova Mulungu wanu, ndine Woyera.
Explore Levitiko 19:2
4
Levitiko 19:17
“ ‘Musamude mʼbale wanu mu mtima mwanu. Koma mudzudzuleni mnzanu moona mtima kuti musakhale wolakwa.
Explore Levitiko 19:17
5
Levitiko 19:31
“ ‘Musamapite kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa owombeza. Musamawafunefune kuti angakuyipitseni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Explore Levitiko 19:31
6
Levitiko 19:16
“ ‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu. “ ‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.
Explore Levitiko 19:16