1
Mlaliki 12:13
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa: uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wa anthu onse.
Compare
Explore Mlaliki 12:13
2
Mlaliki 12:14
Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse, kuphatikizanso zinthu zonse zobisika, kaya zabwino kapena zoyipa.
Explore Mlaliki 12:14
3
Mlaliki 12:1-2
Uzikumbukira mlengi wako masiku a unyamata wako, masiku oyipa asanafike, nthawi isanafike pamene udzanena kuti, “Izi sizikundikondweretsa.” Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala, mwezi ndi nyenyezi zidzada. Mitambo idzabweranso mvula itagwa.
Explore Mlaliki 12:1-2
4
Mlaliki 12:6-7
Kumbukira Iye chingwe cha siliva chisanaduke, kapena mbale yagolide isanasweke; mtsuko usanasweke ku kasupe, kapena mkombero usanathyoke ku chitsime. Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera, mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.
Explore Mlaliki 12:6-7
5
Mlaliki 12:8
“Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki. “Zonse ndi zopandapake!”
Explore Mlaliki 12:8