1
Mlaliki 11:9
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono, ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako. Tsatira zimene mtima wako ukufuna, ndiponso zimene maso ako akuona, koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo Mulungu adzakuweruza.
Compare
Explore Mlaliki 11:9
2
Mlaliki 11:10
Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako, upewe zokupweteka mʼthupi mwako, pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.
Explore Mlaliki 11:10
3
Mlaliki 11:4
Amene amayangʼana mphepo sadzadzala; amene amayangʼana mitambo sadzakolola.
Explore Mlaliki 11:4
4
Mlaliki 11:5
Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo, kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi, momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse.
Explore Mlaliki 11:5
5
Mlaliki 11:6
Dzala mbewu zako mmawa ndipo madzulo usamangoti manja lobodo, pakuti sudziwa chimene chidzapindula, mwina ichi kapena icho, kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.
Explore Mlaliki 11:6
6
Mlaliki 11:2
Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu, pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.
Explore Mlaliki 11:2