Mt. 26
26
Upo wopangana za kupha Yesu
(Mk. 14.1-2; Lk. 22.1-2; Yoh. 11.45-53)
1Yesu atatsiriza kulankhula nkhani zonsezi, adauza ophunzira ake kuti, 2#Eks. 12.1-27“Pajatu chikondwerero cha Paska chiyambika patangopita masiku aŵiri, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti akapachikidwe pa mtanda.”
3Nthaŵi imeneyo akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adasonkhana m'nyumba ya mkulu wa ansembe onse, dzina lake Kayafa. 4Ankakambirana za njira yoti agwirire Yesu mochenjera, nkumupha. 5Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.”
Mai wina adzoza Yesu ku Betaniya
(Mk. 14.3-9; Yoh. 12.1-8)
6Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m'nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate. 7#Lk. 7.37, 38Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira amtengowapatali. Adayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu. 8Koma pamene ophunzira ake adaona zimenezi, adaipidwa nazo nkumauzana kuti, “Chifukwa chiyani kusakaza zinthu chotere? 9Ndithu mafuta ameneŵa akadatha kuŵagulitsa pa mtengo waukulu zedi, kenaka ndalama zake nkukapatsa anthu osauka.”
10Yesu podziŵa zimene iwo aja ankalankhula, adaŵafunsa kuti, “Mukumuvutiranji maiyu? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri. 11#Deut. 15.11Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse. 12Iyeyu wathira mafuta ameneŵa pa thupi langa kuti alidzozeretu lisanaikidwe m'manda. 13Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwinowu pa dziko lonse lapansi, azikafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
Yudasi apangana ndi akulu a Ayuda za kupereka Yesu
(Mk. 14.10-11; Lk. 22.3-6)
14Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe. 15#Zek. 11.12Adakaŵafunsa kuti, “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikadzampereka Yesuyu kwa inu?” Iwo adamupatsa ndalama zasiliva makumi atatu. 16Tsono kuyambira pomwepo iye adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo.
Yesu achita phwando la Paska ndi ophunzira ake
(Mk. 14.12-21; Lk. 22.7-14, 21-23; Yoh. 3.21-30)
17Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?” 18Iye adaŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu kwa munthu wina wake. Mukanene kuti, ‘Aphunzitsi akuti nthaŵi yao ili pafupi, akudzadyera kwanu kuno phwando la Paska pamodzi ndi ophunzira ao.’ ” 19Ophunzira aja adapita nakachita zomwe Yesu adaaŵauza, nakakonzadi za phwando la Paska.
20Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja adakhala pamodzi nkumadya. 21Iwowo alikudya, Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu andipereka kwa adani anga.” 22Ophunzirawo adamva chisoni kwambiri, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti, “Monga nkukhala ine, Ambuye?” 23#Mas. 41.9Yesu adaŵayankha kuti, “Yemwe wasunsa mkate m'mbalemu pamodzi ndi Ine, ameneyo ndiye andipereke. 24Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.” 25Yudasi, amene pambuyo pake adapereka Yesu, adafunsa kuti, “Monga nkukhala ine, Aphunzitsi?” Yesu adamuyankha kuti, “Wanena wekha.”
Za mgonero wa Ambuye
(Mk. 14.22-26; Lk. 22.15-20; 1 Ako. 11.23-25)
26Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, idyani, ili ndi thupi langa.” 27Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu. 28#Eks. 24.8; Yer. 31.31-34Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao. 29Kunena zoona, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano pamodzi nanu mu Ufumu wa Atate anga.”
30Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi.
Yesu aneneratu kuti Petro adzamkana
(Mk. 14.27-31; Lk. 22.31-34; Yoh. 13.36-38)
31 #
Zek. 13.7
Pambuyo pake Yesu adaŵauza kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.’ 32#Mt. 28.16Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.” 33Petro adati, “Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.” 34Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti usiku womwe uno, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.” 35Koma Petro adamuuza kuti, “Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziŵani.” Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi.
Pemphero la Yesu ku Getsemani
(Mk. 14.32-42; Lk. 22.39-46)
36Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikupita uko kukapemphera.” 37Adatengako Petro ndi ana aŵiri aja a Zebedeo.#26.37 ana aŵiri aja a Zebedeo: Onani mau ofotokozera Mt. 20.20. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima. 38Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, komatu mukhale maso pamodzi nane.” 39Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
40Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Mongadi nonsenu mwalephera kukhala maso pamodzi nane ngakhale pa kanthaŵi kochepa? 41Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
42Adachokanso kachiŵiri nakapemphera kuti, “Atate, ngati chikho chamasautsochi sichingandichoke, mpaka nditamwa ndithu, chabwino, zimene mukufuna zichitike.” 43Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera.
44Yesu adaŵasiyanso, napita kukapemphera kachitatu, akunena mau amodzimodzi omwe aja. 45Pambuyo pake adabwera kwa ophunzira ake nati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Ndipotu nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa anthu ochimwa. 46Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.”
Yesu agwidwa
(Mk. 14.43-50; Lk. 22.47-53; Yoh. 18.3-12)
47Yesu akulankhula choncho, wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda. 48Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo, mukamugwire.” 49Tsono Yudasi adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Moni Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona. 50Yesu adamuuza kuti, “Bwenzi langa, chita zimene wadzera.” Apo anthu aja adabwera namugwira Yesu. 51Koma wina mwa amene anali limodzi ndi Yesu, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu. 52Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga. 53Kodi ukuyesa kuti Ine sindingapemphe Atate, Iwo nthaŵi yomweyo nkunditumizira magulu ankhondo a angelo oposa khumi ndi aŵiri? 54Koma ndikadatero, nanga zikadachitika bwanji zimene Malembo adaneneratu kuti ziyenera kuchitika?”
55 #
Lk. 19.47; 21.37 Pamenepo Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kudzandigwira muli ndi malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. 56Koma zonsezi zachitika kuti ziwonekedi zimene aneneri adalemba.”
Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumusiya yekha.
Yesu ku Bwalo Lalikulu la Ayuda
(Mk. 14.53-65; Lk. 22.54-56, 63-71; Yoh. 18.12-14, 19-24)
57Tsono anthu amene adagwira Yesu aja adapita naye kunyumba kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda. 58Koma Petro ankamutsatira chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adaloŵa m'kati, nakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu kuti aone m'mene zithere. 59Akulu a ansembe aja ndi onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni wonama woneneza Yesu kuti amuphe. 60Koma sadaupeze ngakhale padaabwera mboni zambiri zabodza. Potsiriza padabwera anthu aŵiri. 61#Yoh. 2.19Adati, “Munthu uyu ankati, ‘Ine ndingathe kupasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu.’ ”
62Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?” 63Koma Yesu adangokhala chete. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adauza Yesu kuti, “Ndikukulamula m'dzina la Mulungu wamoyo kuti utiwuze molumbira ngati ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu.” 64#Dan. 7.13Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha. Komanso ndikukuuzani kuti kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.” 65#Lev. 24.16Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake nati, “Kunyoza Mulungu koopsatu kumeneku! Kodi pamenepa nkufunanso mboni zina ngati? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku. 66Ndiye inu mukuganiza bwanji?” Iwo aja adayankha kuti, “Ayenera kuphedwa.”
67 #
Yes. 50.6
Pomwepo iwo adayamba kumthira malovu kumaso nkumamumenya, ena kumamuwomba makofi, 68nkumanena kuti, “Iwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, nanga sindiwe mneneri? Lota, wakumenya ndani?”
Petro akana Yesu
(Mk. 14.66-72; Lk. 22.56-62; Yoh. 18.15-18, 25-27)
69Petro adaakhala kunja m'bwalo la nyumba ija. Mtsikana wina wantchito adabwera namuuza kuti, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.” 70Koma iye adakana pamaso pa anthu onse, adati, “Sindikuzidziŵa zimenezo ine.” 71Pamene Petro ankatuluka kumapita ku chipata, mtsikana winanso wantchito adamuwona, nayamba kuuza amene anali pamenepo kuti, “Akulu ameneŵa anali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.” 72Petro adakananso molumbira kuti, “Ndithudi sindikumdziŵa munthu ameneyo.” 73Ndipo patangopita kanthaŵi, anthu amene anali pamenepo adadza nauza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli, tadziŵira kalankhulidwe kakoka.” 74Apo Petro adayamba kulumbira nkumanena kuti, “Mulungu andilange, munthu mukunenayu ine sindimdziŵa konse.” Nthaŵi yomweyo tambala adalira. 75Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo adatuluka, nakalira misozi ndi chisoni chachikulu.
اکنون انتخاب شده:
Mt. 26: BLY-DC
هایلایت
کپی
مقایسه
به اشتراک گذاشتن
می خواهید نکات برجسته خود را در همه دستگاه های خود ذخیره کنید؟ برای ورودثبت نام کنید یا اگر ثبت نام کرده اید وارد شوید
Bible Society of Malawi

: