1
Zek. 6:12
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Tsono umuuze kuti, Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Ndi ameneyutu munthu wotchedwa ‘Nthambi’ uja. Adzaphuka ndi kukulira pomwe aliripo, ndipo adzamangapo Nyumba ya Chauta.
مقایسه
Zek. 6:12 را جستجو کنید
2
Zek. 6:13
Ndiye amene adzamange Nyumba ya Chauta. Ndiye amene adzakhale ndi ukulu waufumu, ndi kumalamulira atakhala pa mpando wake waufumu. Pafupi ndi mpando wake padzakhala wansembe, ndipo aŵiriwo adzagwira ntchito mwamtendere ndi mogwirizana.
Zek. 6:13 را جستجو کنید