1
Zek. 4:6
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga.
مقایسه
Zek. 4:6 را جستجو کنید
2
Zek. 4:10
Pakali pano anthuwo ndi okhumudwa kuwona kuti ntchito sikufulumira. Koma akadzamuwona Zerubabele atatenga mwala wotsiriza uja m'manja mwake, pamenepo adzakondwa. “Nyale zisanu ndi ziŵiri ndi maso a Chauta amene akunka nayang'anayang'ana pa dziko lonse lapansi.”
Zek. 4:10 را جستجو کنید
3
Zek. 4:9
“Zerubabele adamanga maziko a nyumba imeneyi ndi manja ake, adzaitsiriza ndi manja ake omwewo. Motero anthu adzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa iwo.
Zek. 4:9 را جستجو کنید