YouVersion Logo
Search Icon

Matayo 24

24
Yesu wakambilila kugomoledwa kwa nyumba ya Mnungu
Maluko 13:1-2; Luka 21:5-6
1Yesu yapo wadatuluka kubwalo kwa nyumba ya Mnungu, yapo wamachoka oyaluzidwa wake adampitila ni adayamba kukamba naye kuusu nyumba ya Mnungu. 2Yesu wadafujha, “Bwanji, muzipenya izi zonjhe? Zene nikukambilani, palibe ata mwala umojhi uwo siukhalile pamwamba pa wina, kila mwala siugwechedwe panjhi.”
Kulaga ni kuvutika
Maluko 13:3-13; Luka 21:7-19
3Yesu yapo wadakhala pa pili la Mizeituni, oyaluzidwa wake adamchata kwa chisisi, adamfunjha, “Tikambile vindhu ivi sivichike liti? Chizindikilo chanji sichilangize kujha kwako ni mathelo ya jhiko?”
4Yesu wadaayangha, “Chenjelani kuti mundhu waliyonjhe siwadakunyengani. 5Pakuti wandhu ambili saajhe kwa jhina langa niakamba, ‘Ine nde Kilisito,’ ni sianyenge wandhu ambili. 6Simuvele nghani za nghondo ni mbili za nghondo, nambho msadaopa, pakuti yaya yafunika yachokele, nambho mathelo ya jhiko yakali osajhe. 7Wandhu a jhiko limojhi siabulane ni wandhu ajhiko lina, ni wandhu a ufumu umojhi siabulane ni wandhu a ufumu wina. Sikukhale ni njala yaikulu ni chimtingiza cha ndhaka kujhiko lonjhe. 8Yaya yonjheya siyakhale ngati kuyamba kwa kuwawa kwa kupweteka kojhimasula mwana.”
9“Ndiipo sakugwileni kuti mvutichidwe ni kuphedwa. Wandhu a maiko yonjhe siyakuipileni ndande anyiimwe ni oyaluzidwa wanga. 10Nyengo imeneyo, wandhu ambili yawo anikhulupilila siasiye kunikhulupilila, ni kung'anamukana ni kuipilana. 11Siachokele alosi ambili amthila, ni anyiiwo siwanyenge wandhu ambili. 12Ndande ya kuchuluka kwa volakwa, chikondi cha wandhu ambili sichichepe. 13Nambho uyo siwalimbe mbaka pothela, nde uyo siwaomboledwe. 14Uthenga wa bwino uwu siulalikilidwe jhiko lonjhe lapanjhi kuti wandhu wonjhe a pajhiko avele. Nde mathelo yapo siyajhe.”
Masiku ya kuvutika kupunda
Maluko 13:14-23; Luka 21:20-24
15“Chimwecho mukaona ‘Chindhu choipicha icho chipeleka chiwanangiko chaikidwa pa nyumba ya Amnungu’ icho chidakambidwa ni mlosi Danieli.” Chaikidwa pamalo yoyela. Uyo wasoma wajhiwe mate yake! 16“Chimwecho, wajha ali ku jhiko la Yudea athawile ku phili. 17Mundhu waliyonjhe uyo wali kubwalo kwa nyumba yake, siwadalowa mkati kutenga chindhu chilichonjhe. 18Uyo wali ku munda siwadabwela kukhomo kutenga chovala chake. 19Siavutike wajha ali ni pathupi ni yawo ali ni wana akhanda! 20Pembhelani kuti kuthawa kwanu kusadakhala nyengo yo zizila kapina Siku Lopumulila! 21Pakuti nyengo imeneyo sikukhale ni mavuto yayakulu, yayo siyadachokelepo kuyambila jhiko yapo lidaumbidwa mbaka lelo, ni siyachokelanjho mavuto yameneyo. 22Mnungu wadakayachepecha masiku yameneyo ya mavuto, ngati Amnungu wadakasiya kuzichepecha siku zimenezo, palibe uyo wadakakhoza kuomboka. Nambho ndande ya wandhu wake wasangha, Mungu wazichepecha siku zimenezo.”
23“Mundhu waliyonjhe wakakukambilani, ‘Kilisito wali yapa,’ kapina ‘Wali pajha,’ msadamkhuluphilila. 24Sikuchokele ni alosi amthila ni wandhu anyiyawo samakambe mthila kuti anyiiwo achi Kilisito. Siamachite vizindikilo ni vodabwicha vavikulu kuti ikakhozeka wakoke ata anyiwajha asanghidwa. 25Velani, nachogolela kukukambilani nyengo ikali yosafika.”
26“Chimwecho, ngati mundhu waliyonjhe wakukambila, ‘Penya, Kilisito wali kuphululu,’ msadapita kumeneko. Kapina wakakamba, ‘Wali ku chumba,’ msadakhulupila. 27Ngati mbhambe iyo ing'azikila ku mlengalenga ni kuonekana kumwela, ndeumo siikhalile kujha kwa Mwana wa Mundhu.”
28“Paliponjhe pali chitanda nde yapo zisonghana nghwazi.”
Kujha kwa Mwana wa Mundhu
Maluko 13:24-27; Luka 21:25-28
29“Yakathokutha mavuto ya masiku yameneyo, jhuwa silithilidwe mdima, ni mwezi siung'azikila, ndhondwa sizigwe kuchoka ku mlengalenga, ni mbhavu za kumlengalenga sizitingizidwe. 30Ndiipo sipachokele chizindikilo cha Mwana wa Mundhu kumlengalenga ni mafuko yonjhe ya pajhiko siyaimbe nyimbo za zaya. Nawo siamuone Mwana wa Mundhu niwajha pamwamba pamitambo ya kumlengalenga, mu mbhavu ni ulemelelo waukulu. 31Mbetete zazikulu sizipulizidwe, ni iye siwaatume atumiki wake akumwamba ku njhonga zinayi za jhiko lapanjhi. Anyiiwo saike pamojhi wandhu wake yawo asanghidwa kuyambila dela limojhi la jhiko mbaka kudela lina.”
Yaluzo la mtengo uwo utanidwa mtini
Maluko 13:28-31; Luka 21:29-33
32“Jhiyaluzeni chifani ichi kuchokela kwa mtengo wa mtini, ndhawi zake yapo ziyamba kuphukila ni kuchocha machamba, mjhiwa kuti nyengo ya mwavu yawandikila. 33Mchimwechonjho, yapo simuone vindhu vonjhevi, jhiwani kuti ndhawi yakujha Mwana wa Amnungu yawandikila. 34Zenedi nikukambilani, mbadwa uwu siumwalila mbaka yaya yonjhe yapo siyachokele. 35Kumwamba ni pajhiko sivipite, nambho mau yanga siyapita ata pang'ono.”
Palibe uyo wajhiwa siku kapina saa yobwela Mwana wa Mundhu
Maluko 13:32-37; Luka 17:26-30,34-36
36“Palibe mundhu waliyonjhe wajhiwa siku kapina saa ilo siwajhe, osati atumiki akumwamba kapina Mwana, nambho Atate okha nde yawo ajhiwa. 37Kujha kwa Mwana wa Mundhu sikulingane ni chijha chidachokela nyengo ya Nuhu. 38Pa masiku yameneyo ikali osachokele vula ya ikulu, wandhu amadya ni kumwa, waachimuna ni wachikazi amakwata ni kukwatiwa, mbaka yapo Nuhu wadalowa mkati mwa chombo. 39Wandhu achameneo siamajhiwe chalichonjhe icho sichichokele. Vula yambili idagwa ni kwaapha wandhu wonjhe. Chimwecho ndeumo siikhalile yapo siwabwele Mwana wa Mundhu. 40Nyengo imeneyo, waachimuna awili sakhale nialima mmunda, mmojhi siwatengedwe, mwina siwasiidwe. 41Wachikazi awili siakhale pambhelo naapela chakudya, mmojhi siwatengedwe, mwina siwasiidwe. 42Chimwecho mjhipenyelele, pakuti simujhiwa siku lanji ilo siajhe Ambuye wanu. 43Ngati mwene nyumba wadakajhiwa siku lakujha mnghungu, siwadaka gona, siwadakamsiya mnghungu waigomole nyumba yake. 44Chimwecho anyiimwe namwenjho mjhipenyelele, ndande Mwana wa Mundhu siwajhe saa ilo anyiimwe simulijhiwa.”
Mbowa wokhulupilika ni wosakhulupilika
Luka 12:41-48
45Yesu wadaendekela kukamba, “Yani wali mbowa wokhulupilika ni wanjelu? Ni mbowa yujha mbuye wake wamuika kwaimilila mbowa wina, ni kwaapacha chakudya pa saa yabwino. 46Siwakondwele mbowa yujha mbuye wake yapo siwabwele ni kumpheza niwachita chimwecho. 47Zene nikukambila, mkulu wake siwamuike mbowa mmeneyo kukhala woimilila chuma chake. 48Nambho ngati mbowa mmeneyo ni woipa ni wakajhikambila mwene wake, ‘Wamkulu wanga siwachedwe kubwela,’ 49ni kuyamba kwabula mbowa achanjake ni kudya ni kumwa pamojhi ni olojhela. 50Wamkulu wa mbowa yujha siwabwele pa siku ilo siwadaliyembekeze ni pa saa ilo siwadalijhiwe. 51Wamkulu wake mundhu yujha siwamlange kupunda ni kumwika pa gulu limojhi ni wandhu yao samvela. Kumeneko sikukhale chililo ni kukukuta mano.”

Currently Selected:

Matayo 24: NTNYBL2025

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in