Yohana 14
14
Yesu ni Njila yopita kwa Atate
1Yesu waadakambila, “Simudadandaula mumitima yanu. Mwaakhulupilila Amnungu, munikhulupilile ni ine. 2Munyumba ya Atate wanga muli ni makhalo yambili, ngati siidakali chimwecho, nidakakukambilani. Chipano nipita kukukonjelani malo. 3Nikapita kukukonjelani malo, sinibwele kukutengani mujhe kwanga, yapo nili ine namwe mukhalepo. 4Anyiimwe mujhiwa mapitidwe ya uko nipita.”
5Tomaso wadamfunjha, “Ambuye, uko mpita ife sitikujhiwa, sitiijhiwe bwanji njila yopita kumeneko?”
6Ndiipo Yesu wadamuyangha, “Ine namwene nde njila, naakambila wandhu uzene ni kwapacha umoyo wa muyaya. Palibe uyo wakhoza kupita kwa Atate ila kwanjila yanga. 7Ngati munijhiwa ine, simwajhiwe ni Atate wanga. Ni kuyambila chipano, mwajhiwa, ni mwatho kwaona.”
8Filipo wadamkambila Yesu, “Ambuye tilangizeni Atate, kwatu ikwana.”
9Yesu wadamkambila, “Filipo nakhala namwe ndhawi yonjheyi, ukali osanijhiwe? Uyo waniona ine waona Atate. Ukamba bwanji, ‘Tilangizeni Atate?’ 10Bwanji, siukhulupilila kuti ine nili mkati mwa Atate, ni Atate ali mkati mwanga? Mawu yayo nikukambilani osati kwa lamulo langa, Atate yawo alimkati mwanga achita njhito zao. 11Ifunika munikhulupilile yapo nikamba nili mkati mwa Atate ni Atate alimkati mwanga. Ngati osati chimwecho mnikhulupilile kwa njhito izo nizichita. 12Zene nikukambilani, uyo wanikhulupilila siwachite vindhu ivo nichita ine, ni siwachite vavikulu kupunda, ndande nipita kwa Atate. 13Chilichonjhe icho simupembhe ngati umo nifunila sinichite, dala Atate apachidwe ulemelelo mkati mwa Mwana. 14Mkanipembha chilichonjhe ngati umo nifunila, sinikuchitileni.”
Yesu waahidi kumpeleka Mzimu woyela
15“Ngati mnikonda malamulo yanga yawo nikupachani simuya chitile njhito. 16Sinaapembhe Atate nawo sakupacheni Wakukuthandizani mwina, uyo siwakhale namwe muyaya. 17Iye ni Mzimu wa zene. Jhiko lapanjhi silikhoza kumlandila ndande silimuona kapina kumjhiwa. Nambho anyiimwe mumjhiwa ndande wakhala namwe ni wali mkati mwanu.”
18“Sinikusiyani amasiye, sinijhenjho kwanu. 19Ikali ndhawi yochepa wandhu ajhiko la panjhi sanionanjho, nambho anyiimwe simunione, pakuti ine nili wamoyo namwenjho simukhale moyo. 20Ndhawi ijha ikafika simujhiwe kuti ine nilimkati mwa Atate, namwe muli mkati mwanga ni ine nilimkati mwanu.”
21“Uyo wayalandila malamulo yanga ni kuyagwila, mmeneyo nde uyo wanikonda. Uyo wanikonda ine siwakondedwe ni Atate wanga, nane sinimkonde ni kujhijhiwicha kwa iye.”
22Chimwecho Yuda nambho osati Isikaliyote adamkambila, “Ambuye, sikhozeke bwanji mujhilangize kwa ife ni osati kwa jhiko?”
23Yesu wadayangha, “Wandhu yao anikonda akalichitila njhito mawu langa ni Atate wanga saakonde, nafe sitijhe kwa anyiiwo ni kukhala pamojhi nawo. 24Uyo siwanikonda siwayachitila njhito mawu yanga. Uthenga uwo muuvela osati wanga nambho uchokela kwa Atate yao anituma.”
25“Nikuyaluzani vindhu ivi nikali pamojhi namwe, 26nambho Othandiza, Mzimu woyela, uyo samtume kukhala mmalo mwanga, siwakuyaluzeni kila kandhu ni kukukumbuchani yonjhe yayo nakukambilani.”
27“Mtendele nikusiilani, nikupachani mtendele wanga. Yetu nikupachani osati ngati umo likupachilani jhiko la panjhi. Simudakhaikila mumtima ni simdaopa. 28Mudanivela yapo nimakamba, ‘Nipita ni sinibwelenjho kwanu.’ Ngati mdanikonda, mdakakondwa ndande nipita kwa Atate, mateyake iwo wakulu kusiyana niine. 29Chipano nakukambilani yakali yosa chokele, ndande yapo siyachokele mukhulupilile. 30Sinikamba namwenjho kopitilila, ndande mlamuli wa jhiko lino watokujha, kwaine siwakhoza kandhu, 31nambho wandhu ajhiko lino afunika kujhiwa kuti ine naakonda Atate, nde ndande nichita ngati umo anilamulila Atate.”
“Imani tijhipita!”
Currently Selected:
Yohana 14: NTNYBL2025
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.