YouVersion Logo
Search Icon

Mt. 20

20
Fanizo la antchito olembedwa pa nthaŵi zosiyana
1“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaalaŵirira m'mamaŵa kukalemba anthu okagwira ntchito m'munda wake wamphesa. 2Adaapangana nawo kuti adzaŵalipira ndalama imodzi yasiliva pa tsiku, naŵatuma kumunda kwake. 3Pa nthaŵi ya 9 koloko adapitanso, nakapeza ena atangokhala khale pa msika, osagwira ntchito. 4Adaŵauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa, ndidzakulipirani moyenerera.’ 5Iwowo adapitadi. Munthu uja adapitanso pa 12 koloko masana ndi pa 3 koloko, nakachita chimodzimodzi. 6Pafupi 5 koloko madzulo adapitanso nakapeza enanso akungokhala. Adaŵafunsa kuti, ‘Bwanji mwangokhala khale pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ 7Iwowo adayankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba.’ Iye uja adaŵauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa.’
8 # Lev. 19.13; Deut. 24.15 “Dzuŵa likuloŵa, mwinimunda uja adauza kapitao wake kuti, ‘Kaŵaitane antchito aja, uŵalipire. Uyambire amene alembedwa potsirizawo, utsirizire oyamba aja.’ 9Pamene adabwera olembedwa pa 5 koloko yamadzulo aja, aliyense adalandira ndalama imodzi. 10Tsono pamene olembedwa poyamba aja adabwera, ankaganiza kuti alandira pakulu. Koma nawonso adangolandira aliyense ndalama imodzi. 11Ndiye iwowo polandira, adayamba kuŵiringula, 12adati, ‘Aa! Anzathu otsiriziraŵa angogwira ntchito kanthaŵi pang'ono, bwanji mwaŵapatsa malipiro olingana ndi athu, pamene ifeyo tathyoka nayo ntchito tsiku lathunthu, ndi chidzuŵa chonse chija?’ 13Koma mwinimunda uja adayankha mmodzi mwa iwo kuti, ‘Iwe, inetu sindidakubere ai. Kodi suja tinapangana ndalama yasiliva imodzi? 14Tenga malipiro ako, uzipita. Mwiniwakene ndafuna kuti ndipatse wolembedwa potsirizayu molingana ndi iwe. 15Kodi zinthu zanga ndisachite nazo monga ndifunira? Kapenatu ukuipidwa nawo ufulu wanga eti?’ ”
16 # Mt. 19.30; Mk. 10.31; Lk. 13.30 Tsono Yesu adati, “Choncho amene ali oyambirira adzakhala otsirizira. Ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”
Yesu aneneratu kachitatu za kufa ndi kuuka kwake
(Mk. 10.32-34; Lk. 18.31-34)
17Pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, adaŵatengera pambali ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. Pa njira adaŵauza kuti, 18“Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe, 19ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamkwapula, nkumupachika pa mtanda; koma mkucha wake Iye adzauka kwa akufa.”
Zopempha za mai
(Mk. 10.35-45; Lk. 22.24-27)
20Pambuyo pake mkazi wa Zebedeo adadza ndi ana ake#20.20: Ana ake: Ameneŵa ndi Yakobe ndi Yohane (Mt. 4.21). kwa Yesu, namgwadira kuti ampemphe kanthu. 21Yesu adamufunsa kuti, “Amai, kodi muli ndi mau?” Iye adayankha kuti, “Ndimati mulonjeze kuti mu Ufumu wanu ana anga aŵiriŵa adzakhale wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.” 22Koma Yesu adayankha kuti, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine?” Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.” 23Apo Yesu adati, “Chabwino, mudzamwa nao chikho changacho. Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Atate ndiwo adzapereke malo ameneŵa kwa amene Atatewo adaŵakonzera.”
24Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima abale aŵiri aja. 25#Lk. 22.25, 26Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti olamulira amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao. 26#Mt. 23.11; Mk. 9.35; Lk. 22.26Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. 27Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu. 28Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Yesu achiritsa anthu aŵiri akhungu
(Mk. 10.46-52; Lk. 18.35-43)
29Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankatuluka mu mzinda wa Yeriko, anthu ambirimbiri ankamutsatira. 30Panali anthu aŵiri akhungu amene adaakhala pansi pamphepete pa mseu. Iwo aja atamva kuti Yesu akupita mumseumo, adayamba kufuula kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.” 31Anthu aja adaŵazazira akhunguwo kuti akhale chete. Koma iwo nkumafuulirafuulira kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.” 32Yesu adaima, naŵaitana, nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” 33Iwo aja adati, “Ambuye, tikufuna kuti tizipenya.” 34Yesu adaŵamvera chifundo nakhudza maso ao. Pompo iwo adayamba kupenya, kenaka nkumamutsata.

Currently Selected:

Mt. 20: BLY-DC

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in