Mt. 13
13
Fanizo la wofesa mbeu
(Mk. 4.1-9; Lk. 8.4-8)
1Tsiku lomwelo Yesu adatuluka m'nyumba nakakhala pansi m'mbali mwa nyanja. 2#Lk. 5.1-3Anthu ambirimbiri adasonkhana kumene kunali Iye. Tsono Yesu adaloŵa m'chombo nakhala pansi, anthu onse aja ataima pa mtunda. 3Yesu adalankhula nawo zambiri m'mafanizo.
Adati, “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. 4Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira, ndipo mbalame zidabwera nkuzitolatola. 5Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga chifukwa nthakayo inali yosazama. 6Koma pamene dzuŵa lidakwera, zidapserera kenaka zidauma, chifukwa zinali zosazika mizu. 7Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija. 8Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi khumi, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi atatu.” 9Tsono Yesu adati, “Amene ali ndi makutu, amve!”
Za cholinga cha mafanizo
(Mk. 4.13-20; Lk. 8.11-15)
10Pambuyo pake ophunzira a Yesu aja adadzamufunsa kuti, “Kodi bwanji anthuŵa mumalankhula nawo m'mafanizo?” 11Iye adati, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wakumwamba. Koma enaŵa sadaŵaululire ai. 12#Mt. 25.29; Mk. 4.25; Lk. 8.18; 19.26Pajatu amene ali nkanthu kale, adzampatsanso zina, nadzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe kanthu, adzamlanda ngakhale kakang'onong'ono kamene ali nako. 13Tsono anthuŵa ndimalankhula nawo m'mafanizo, chifukwa ngakhale amapenya, komabe saona, ndipo ngakhale amamva, komabe samva kwenikweni kapena kumvetsa. 14#Yes. 6.9, 10 Ndi iwoŵa zikuchitikadi zimene mneneri Yesaya adaanena kuti,
“ ‘Kumva mudzamva ndithu, koma osamvetsa,
kuyang'ana mudzayang'ana ndithu, koma osapenya.
15Ndithu anthu ameneŵa nzeru zao nzobuntha,
adagonthetsa makutu ao,
ndipo adapsinya maso ao,
kuwopa kuti angamapenye ndi maso aowo,
angamamve ndi makutu aowo,
angamamvetse ndi nzeru zaozo,
ndi kutembenuka mtima,
Ineyo nkuŵachiritsa.’
16 #
Lk. 10.23, 24 “Koma inu ndinu odala, popeza kuti maso anu akupenya, ndipo makutu anu akumva. 17Kunena zoona aneneri ambiri ndi anthu ambiri olungama, adaafunitsitsa kuwona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adaafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.”
Tanthauzo la fanizo la wofesa mbeu
(Mk. 4.13-20; Lk. 8.11-15)
18“Tsono inu mumvetse bwino tanthauzo lake la fanizo la munthu wofesa mbeu lija. 19Munthu aliyense akamva mau onena za Ufumu wakumwamba, koma osaŵamvetsa, Woipa uja amabwera nkudzalanda zimene zidafesedwa mumtima mwake. Zimenezi ndiye mbeu zogwera m'njira zija. 20Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe. 21Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo munthuyo amabwerera m'mbuyo. 22Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu. Koma kutanganidwa ndi za pansi pano ndi kukondetsa chuma kumafooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso. 23Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu naŵamvetsa. Munthu wotere amaberekadi zipatso, mwina makumi khumi, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi atatu.”
Fanizo la namsongole pakati pa tirigu
24Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaafesa mbeu zabwino m'munda mwake. 25Koma anthu onse ali m'tulo, mdani wake adabwera, nkufesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. 26Tsono pamene mmera udakula nkuyamba kuchita njere, namsongole uja nayenso adayamba kuwoneka. 27Antchito a mwinimunda uja adadzamufunsa kuti, ‘Bwana, kodi suja mudaafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga bwanji mukuwonekanso namsongole?’ 28Iye adaŵayankha kuti, ‘Ndi mdani amene wachita zimenezi.’ Antchito aja adamufunsa kuti, ‘Bwanji tikamzule?’ 29Koma iye adati, ‘Iyai, mungakazulire kumodzi ndi tirigu pozula namsongoleyo. 30Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthaŵi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m'mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m'nkhokwe yanga.’ ”
Fanizo la njere ya mpiru ndi la chofufumitsira buledi
(Mk. 4.30-34; Lk. 13.18-21)
31Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake. 32Ndi yaing'ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina zonse. Komabe mbeu yake ikakula, imapambana zitsamba zina zonse. Imasanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.”
33Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.”
34Zonsezi Yesu adalankhula ndi anthu aja m'mafanizo. Sadalankhule nawo kanthu popanda fanizo. 35#Mas. 78.2Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti,
“Ndidzalankhula nawo m'mafanizo.
Ndidzaulula zimene zinali zobisika
chilengedwere dziko lapansi.”
Tanthauzo la fanizo la namsongole pakati pa tirigu
36Pambuyo pake Yesu adaŵasiya anthu ambirimbiri aja, nakaloŵa m'nyumba. Tsono ophunzira ake adadzampempha kuti, “Tatimasulirani fanizo la namsongole wam'munda lija.” 37Yesu adati, “Wofesa mbeu zabwino uja ndi Mwana wa Munthu. 38Munda uja ndi dziko lino lapansi. Mbeu zabwino zija ndi anthu ake a Ufumu wakumwamba. Namsongole uja ndi anthu ake a Woipa uja. 39Mdani wodzafesa namsongole uja ndi Satana. Kudula kuja nkutha kwake kwa dziko lino lapansi, ndipo odula aja ndi angelo. 40Monga momwe adaazulira namsongole uja nkumutentha pa moto, zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. 41Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa, 42nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano. 43#2Es. 7.97Tsono anthu olungama adzaŵala ngati dzuŵa mu Ufumu wa Atate ao. Amene ali ndi makutu, amve!
Fanizo la chuma chobisika ndi la ngale yamtengowapatali
44“Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m'munda. Munthu wina atachitumba, amachibisanso. Kenaka mokondwa amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda uja.
45“Ndiponso Ufumu wakumwamba uli ngati munthu wamalonda wonka nafunafuna ngale zokongola zamtengowapatali. 46Atapeza ngale imodzi yamtengowapatali kwambiri, amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula ngale ija.
Fanizo la khoka
47“Ufumu wakumwamba ulinso ngati khoka limene anthu amaliponya m'nyanja, ndipo limagwira nsomba za mitundu yonse. 48Likadzaza, anthu amalikokera ku mtunda. Tsono amakhala pansi, nsomba zabwino nkumaziika m'madengu, zachabe nkumangozitaya. 49Zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Angelo adzabwera nadzachotsa anthu ochimwa pakati pa anthu olungama, 50nkumaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”
Za chuma chatsopano ndi chakale
51Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Mwazimvetsa zonsezi kodi?” Iwo adati, “Inde.” 52Apo Iye adaŵauza kuti, “Nchifukwa chaketu mphunzitsi aliyense wa Malamulo, amene adaphunzira za Ufumu wakumwamba, ali ngati mwinibanja amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zinthu zakale m'nkhokwe ya chuma chake.”
Anthu amkana Yesu ku Nazarete
53Yesu atatsiriza kunena mafanizoŵa, adachoka kumeneko. 54Atafika ku dera lakwao#13.54 dera lakwao: Onani mau ofotokozera 9.1, adayamba kuphunzitsa anthu m'nyumba yao yamapemphero. Amene ankamumva ankadabwa nkumati, “Kodi Iyeyu, nzeru zimenezi ndi mphamvuzi adazitenga kuti? 55Kodi ameneyu si mwana wa mmisiri wa matabwa uja? Kodi suja mai wake ndi Maria? Ndipo abale ake si Yakobe, Yosefe, Simoni ndi Yuda? 56Kodi suja alongo ake onse ali nafe pompano? Nanga tsono zonsezi adazitenga kuti?” 57#Yoh. 4.44Choncho adakhumudwa naye. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao ndiponso kubanja kwao.” 58Motero sadachite zamphamvu zambiri kumeneko, chifukwa cha kusakhulupirira kwa anthuwo.
Currently Selected:
Mt. 13: BLY-DC
Highlight
Copy
Compare
Share
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi