YouVersion Logo
Search Icon

Mal. 3

3
1 # Mt. 11.10; Mk. 1.2; Lk. 1.76; 7.27 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzatuma wamthenga wanga kuti akandikonzere njira. Kenaka mwadzidzidzi Chauta amene mukumfunafuna adzafika ku Nyumba yake. Wamthenga wa chipangano, amene mukumuyembekeza, suuyu akubwera. 2#Yow. 2.11; Chiv. 6.17 Kodi ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Kodi ndani adzatha kulimbikira iye akadzafika?
“Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wapang'anjo, ndiponso ngati sopo wa munthu wochapa. 3Adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri wapang'anjo woyeretsa siliva, ndipo adzayeretsa Alevi monga amayeretsera golide ndi siliva, mpaka kuti azidzapereka nsembe zoyenera kwa Chauta. 4Choncho nsembe za Yuda ndi za Yerusalemu zidzakondweretsa Chauta, monga zidaaliri masiku amakedzana.”
5Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsono ndidzakufikani pafupi kuti ndikuzengeni mlandu. Mosataya nthaŵi ndidzanena mau otsutsa mfiti, anthu achigololo, a umboni wonama, odyerera antchito ao, ovutitsa akazi ndi ana amasiye, ochita alendo zosalungama ndipo onse amene sandiwopa Ine.
Za kupereka mitulo
6 # Mphu. 48.10 “Ine ndine Chauta, wosasinthika. Nchifukwa chake inu zidzukulu za Yakobe simudaonongeke. 7Kuyambira masiku a makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga, simudaŵatsate konse. Ngati mubwerera kwa Ine, Inenso ndidzabwerera kwa inu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Komabe inu mumati, ‘Kodi tingathe kubwerera bwanji?’ 8Ine ndikuti, Kodi munthu angathe kubera Mulungu? Komabe inu mumandibera. Inu mumati, ‘Kodi timakuberani bwanji?’ Ine ndikuti, Mumandibera pa zachikhumi zanu ndi zopereka zina. 9Ndinu otembereredwa nonsenu, mtundu wanu wonse, chifukwa choti mumandibera. 10#Lev. 27.30; Num. 18.21-24; Deut. 12.6; 14.22-29; Neh. 13.12 Aliyense abwere ndi chachikhumi chathunthu ku Nyumba yanga, kuti m'menemo mukhale chakudya chambiri. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Mundiyese tsono, ndipo muwone ngati sinditsekula zipata zakumwamba ndi kukugwetserani madalitso ochuluka. 11Ndidzaletsa tizilombo kuti tisadye mbeu zanu, mipesa yanu sidzaleka kubala. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. 12Motero anthu a mitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
13Chauta akunena kuti, “Mwalankhula mau olasa onena Ine. Komabe mukuti, ‘Kodi takunenani zotani?’ 14Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nkwachabe. Kodi pali phindu lanji kumatsata malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, kapena kumaonetsa chisoni pamaso pake? 15Koma ife timayesa kuti anthu odzikuza ndiwo odala. Anthu ochita zoipa ndiwo amene amakhala pabwino, ngakhale akaputa Mulungu amapulumuka ndithu.’ ”
Za tsiku la Chauta
16Tsono oopa Chauta adayamba kukambirana, Chauta namamvetsera. Buku lachikumbutso lidalembedwa pamaso pake, lonena za amene ankaopa Chauta ndi kulemekeza dzina lake. 17Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, adzakhala angaanga okondedwa pa tsiku limene ndidzalikonza. Ndidzaŵachitira chifundo monga m'mene munthu amachitira ndi mwana wake womtumikira. 18Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu abwino ndi anthu oipa, pakati pa anthu otumikira Mulungu ndi osamtumikira.”

Currently Selected:

Mal. 3: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy