Skip to content

Ntc. 10

10
Za Petro ndi Kornelio
1Ku Kesareya kunali munthu wina, dzina lake Kornelio. Iyeyu anali mkulu wa asilikali 100 achiroma, a m'gulu lotchedwa “Gulu la ku Italiya.” 2Anali munthu wotsata zachipembedzo, ndipo iye pamodzi ndi banja lake lonse ankaopa Mulungu. Ankathandiza kwambiri Ayuda osauka, ndipo ankapemphera Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi. 3Tsiku lina dzuŵa litapendeka, nthaŵi ili ngati 3 koloko, adaona zinthu m'masomphenya. Adaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu akubwera kwa iye nkunena kuti, “Kornelio!” 4Iye adayang'anitsitsa mngeloyo mantha atamgwira, ndipo adamufunsa kuti, “Nkwabwino, Ambuye?” Mngeloyo adati, “Mulungu wakondwera nawo mapemphero ako ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo zako. 5Tsopano tuma anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina, dzina lake Simoni, wotchedwanso Petro. 6Akukhala kwa Simoni wina, mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja.” 7Mngelo amene ankalankhula naye uja atachoka, Kornelio adaitana antchito ake aŵiri, ndiponso msilikali. Msilikaliyo anali mmodzi mwa amene ankamutumikira, ndipo anali munthu wopembedza Mulungu. 8Kornelio uja ataŵafotokozera zonse, adaŵatuma ku Yopa.
9 # Yud. 8.5 M'maŵa mwake, iwo aja akali m'njira koma akuyandikira mudziwo, Petro adakwera pa denga kukapemphera, nthaŵi ili ngati 12 koloko masana. 10Ali pamenepo, adamva njala, namafuna kudya. Koma pamene anthu ankakonza chakudya, iye adachita ngati wakomoka. 11Adaona kuthambo kutatsekuka, chinthu china chikutsikira pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai. 12M'menemo munali nyama zamitundumitundu, ndi zokwaŵa, ndiponso mbalame zamumlengalenga. 13Tsono Petro adamva mau akuti, “Petro dzuka, ipha udye.” 14Koma Petro adati, “Iyai, pepani Ambuye, ine sindinadyepo ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa.” 15Kenaka Petro adamvanso kachiŵiri mau akuti, “Zimene Mulungu waziyeretsa, iwe usati nzosayera.” 16Zimenezi zidachitika katatu, ndipo pompo chinthu chija chidatengedwa kupitanso kumwamba.
17Petro adayamba kusinkhasinkha za tanthauzo la zimene adaaziwona m'masomphenya zija. Nthaŵi yomweyo anthu amene Kornelio adaaŵatuma aja, ankafunsa za nyumba ya Simoni, ndipo tsopano adaadzaima pa khomo. 18Adaitana nkufunsa kuti, “Kodi kuli mlendo kuno, dzina lake Simoni, wotchedwanso Petro?” 19Pamene Petro ankalingalirabe za zimene adaaziwona m'masomphenya zija, Mzimu Woyera adamuuza kuti, “Iwe, anthu atatu akukufuna. 20Nyamuka, tsika, upite nawo osakayika, pakuti ndaŵatuma ndine.” 21Apo Petro adatsika nauza anthu aja kuti, “Amene mukumfunayo ndine. Kodi nkwabwino?” 22Iwo adati, “Kornelio, mkulu wa gulu la asilikali 100, watituma. Iyeyo ndi munthu wolungama ndi woopa Mulungu, ndipo Ayuda onse amamtama. Mngelo wa Mulungu adamuuza kuti akuitaneni kuti mupite kunyumba kwake akamve mau amene muli nawo.” 23Pamenepo Petro adaŵaloŵetsa m'nyumba, naŵasamala.
M'maŵa mwake adanyamuka napita nawo, ndipo abale ena a ku Yopa adamperekeza. 24M'maŵa mwake adafika ku Kesareya. Kornelio ankaŵadikira, atasonkhanitsa abale ndi abwenzi ake apamtima. 25Pamene Petro ankati aziloŵa, Kornelio adadzakumana naye, nadzigwetsa kumapazi kwake, namuŵeramira. 26Koma Petro adamuimiritsa nati, “Iyai, imirirani, inenso ndine munthu chabe.” 27Ndipo akulankhula naye, adaloŵa napeza anthu ambiri atasonkhana. 28Pamenepo Petro adaŵauza kuti, “Inu nomwe mukudziŵa kuti Myuda saloledwa konse kuyanjana ndi munthu wa mtundu wina, ngakhale kuloŵa m'nyumba mwake. Koma Mulungu wandidziŵitsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ngwosayera kapena wonyansa. 29Nchifukwa chake ndabwera mosaŵiringula pamene mudandiitana. Tsono ndimati ndidziŵe chimene mwandiitanira.”
30Kornelio adati, “Dzana ilo, ndinkapemphera m'nyumba mwanga, nthaŵi ngati yomwe ino ya 3 koloko dzuŵa litapendeka. Mwadzidzidzi kutsogolo kwangaku kudaimirira munthu wovala zovala zonyezimira. 31Adandiwuza kuti, ‘Kornelio, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo. 32Tsono tuma anthu ku Yopa akaitane Simoni wotchedwa Petro. Iyeyu akukhala kwa Simoni, mmisiri wa zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa njanja.’ 33Nchifukwa chake ndidaakutumirani anthu msanga, ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akulamulani kuti munene.”
Mau a Petro m'nyumba ya Kornelio
34 # Deut. 10.17 Petro adayamba kulankhula, adati, “Zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. 35Amalandira bwino munthu wa mtundu uliwonse womuwopa nkumachita chilungamo. 36Mukudziŵa kuti adatumizira Aisraele mau ake naŵauza Uthenga Wabwino wa mtendere kudzera mwa Yesu Khristu, amene ali Ambuye a anthu onse. 37Mukudziŵa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthaŵi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. 38Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana. 39Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m'dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda. 40Komabe mkucha wake Mulungu adamuukitsa kwa akufa, nalola kuti aonekere poyera.#10.40: nalola…poyera: Onani mau ofotokozera Ntc. 1.3. 41Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa. 42Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe. 43Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”
Anthu a mitundu ina alandira Mzimu Woyera
44Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adaŵatsikira anthu onse amene ankamva mauwo. 45Ndipo okhulupirira achiyuda amene adaaperekeza Petro, adadabwa kuti Mulungu adapereka mphatso ya Mzimu Woyera ndi kwa anthu akunja omwe. 46Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati, 47“Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?” 48Motero adalamula kuti abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Ndipo anthuwo adampempha kuti akhale nawo masiku angapo.