YouVersion Logo
Search Icon

YUDA 1

1
1 # Luk. 6.16; Yoh. 17.11-12, 15 Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu: 2#1Pet. 1.2Chifundo ndi mtendere ndi chikondi zikuchulukireni.
Atsutsa aphunzitsi onyenga
3 # Afi. 1.27 Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima. 4#Aro. 9.21-22; Tit. 1.16Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.
5 # 1Ako. 10.9 Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira. 6#Yoh. 8.44; 2Pet. 2.4Angelonso amene sanasunga chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala paopao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu. 7#Gen. 19.24Monga Sodomu ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha. 8#2Pet. 2.10Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero. 9#Dan. 12.1; Zek. 3.2; Chiv. 12.7Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule. 10#2Pet. 2.12Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika. 11#Gen. 4.5-8; Num. 16.1-35; 22.7, 21Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora. 12#1Ako. 11.21; 2Pet. 2.17Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu; 13#Afi. 3.19; 2Pet. 2.13-17mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha. 14#Gen. 5.18; Mat. 25.31Ndipo kwa iwo, Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, 15#Mat. 25.31kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye. 16#2Pet. 2.18; Yak. 2.1, 9Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.
17Koma inu, abale, mukumbukire mau onenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu; 18#1Tim. 4.1kuti ananena nanu, Pa nthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo okha. 19#Hos. 9.10Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe achibadwidwe, osakhala naye Mzimu.
Machenjezo; mayamiko kwa Mulungu
20 # Aro. 8.26; Akol. 2.7 Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, 21#Tit. 2.13mudzisunge nokha m'chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha. 22Ndipo ena osinkhasinkha muwachitire chifundo, 23#Amo. 4.11; Zek. 3.4koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane naonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi. 24#Aef. 3.20; Akol. 1.22Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera, 25#Aro. 16.27; 1Tim. 1.17; 2.3kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, zikhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.

Currently Selected:

YUDA 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in