YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba
Mneneri Yeremiya adalalikira kwa zaka zambiri, mzinda wa Yerusalemu usanapasuke (586 BC), ndiponso zaka zina zingapo mzindawo utapasuka. Mau ake ambiri ngochenjeza Ayuda akuti likubwera tsiku pamene Mulungu adzawalanga ndi kuwononga Yerusalemu, chifukwa cha machimo ao ndi kupembedza milungu ina. Tsono zimenezi zidachitikadi pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adadzazinga mzindawo nkuwuononga pamodzi ndi Kachisi wa Yehova; anthu ake ambiri pamodzi ndi mfumu yomwe adawatenga ukapolo nkupita nawo ku Babiloni, Yeremiya uja akuwona. Iye adalankhulanso mau ena onena kuti tsiku lina anthu otengedwa ku ukapolowo adzabwerera kwao ndi kukhalanso pabwino.
Yeremiya anali munthu wachifundo, wokonda Ayuda anzake kwambiri; ankawamvera chisoni ndipo nchifukwa chake ankayenera kuwadzudzula ndi kuwachenjeza. Mau ake aonetsa kuti ntchito imene Yehova adamupatsa inkawawitsa mtima wake. Mau a Yehova ankayaka ngati moto mumtima mwake, kotero kuti sankathanso kusunga mauwo mumtima mwake mpaka atalengeza zonse.
Mau ena a m'bukuli aloza zakutsogolo pamene Yehova adzakhazika chipangano chatsopano, cholembedwa m'mtima ya anthu, mwakuti anthuwo sadzasowanso mphunzitsi wowakumbutsa zimenezi (31.31-34).
Za mkatimu
Bukuli lili ndi zigawo zingapo:
Kuitanidwa kwa Yeremiya 1.1-19
Mau a Yehova kwa atsogoleri ao 2.1—25.38
Mau ena a Yehova ndipo zochitika zina ndi zina 26.1—45.5
Mau ena otsutsa mitundu ina ya anthu 46.1—51.64
Mau oonjezera osimba za kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu 52.1-34

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy