YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 3

3
1 # Deut. 24.1-4; Mas. 106.38; Zek. 1.3 Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova. 2#Mas. 106.38Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagona ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m'chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako. 3#Deut. 28.23-24Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi. 4#Miy. 2.17Kodi kuyambira tsopano sudzafuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu? 5#Mas. 103.9; Yes. 57.16Kodi adzasunga mkwiyo wake kunthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka chimaliziro? Taona, wanena ndi kuchita zoipa monga unatero.
Abwere kwa Yehova anthu olowererawo
6 # Yer. 3.11, 14 Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri atali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo. 7#2Maf. 17.13Ndipo ndinati atachita zimenezo zonse, Adzabwera kwa Ine; koma sanabwere, ndipo mphwake wonyenga, Yuda, anaona. 8#2Maf. 17.6, 8; Ezk. 23.4, 11Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata wachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama. 9Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo. 10Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova. 11#Yer. 3.14Ndipo Yehova anati kwa ine, Israele wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga. 12#Mas. 86.15Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse. 13#Miy. 28.13Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvera mau anga, ati Yehova. 14#Aro. 11.5Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzimmodzi wa pa mudzi uliwonse, ndi awiriawiri a pa banja lililonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni; 15#Ezk. 34.23; Aef. 4.11ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha. 16Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kuchuluka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la chipangano cha Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzachitanso konse. 17#Yes. 60.9Pa nthawi yomweyo adzatcha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa. 18#Ezk. 37.16-22Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderena ndi nyumba ya Israele, ndipo adzatuluka pamodzi kudziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo. 19#Yes. 63.16Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine. 20#Yes. 48.8Ndithu monga mkazi achokera mwamuna wake monyenga, chomwecho mwachita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israele, ati Yehova. 21Mau amveka pa mapiri oti see, kulira ndi kupempha kwa ana a Israele; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao. 22#Yer. 3.14; Hos. 6.1Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu. 23#Mas. 3.8; 121.1-2Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele. 24#Hos. 9.10Ndipo chochititsa manyazi chinathetsa ntchito za atate athu kuyambira ubwana wathu; nkhosa zao ndi zoweta zao, ana ao aamuna ndi aakazi. 25#Ezr. 9.7Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvera mau a Yehova Mulungu wathu.

Currently Selected:

YEREMIYA 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy